Ndipo anauza mfumu ya Aejipito kuti anthu adathawa; ndi mtima wa Farao ndi wa anyamata ake inasandulikira anthuwo, ndipo anati, Ichi nchiyani tachita, kuti talola Israele amuke osatigwiriranso ntchito?
Eksodo 8:15 - Buku Lopatulika Koma pamene Farao anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wake, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Koma pamene Farao anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wake, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Farao ataona kuti zinthu zayamba kukhala bwino, adaumitsa mtima wake, ndipo sadafunenso kumvera Mose ndi Aroni monga momwe Chauta adaanenera muja. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Koma Farao ataona kuti zinthu zinayambanso kukhala bwino, anawumitsanso mtima wake ndipo sanamverenso mawu a Mose ndi Aaroni, monga momwe Yehova ananenera. |
Ndipo anauza mfumu ya Aejipito kuti anthu adathawa; ndi mtima wa Farao ndi wa anyamata ake inasandulikira anthuwo, ndipo anati, Ichi nchiyani tachita, kuti talola Israele amuke osatigwiriranso ntchito?
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kunka ku Ejipito, usamalire uchite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wake kuti asadzalole anthu kupita.
Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aejipito, ndipo ndidzatulutsa makamu anga, anthu anga ana a Israele, m'dziko la Ejipito ndi maweruzo aakulu.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Nena ndi Aroni, Samula ndodo yako, nupande fumbi lapansi, kuti lisanduke nsabwe m'dziko lonse la Ejipito.
Ndipo Farao anati, Ndidzakulolani mumuke, kuti mukamphere nsembe Yehova Mulungu wanu m'chipululu; komatu musamuke kutalitu: mundipembere.
Ndipo Mose anati, Onani, ndilikutuluka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza ichoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ake, ndi kwa anthu ake; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova.
Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andichotsere ine ndi anthu anga achulewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe.
Yemwe aumitsa khosi atadzudzulidwa kwambiri, adzasweka modzidzimuka, palibe chomchiritsa.
Popeza sambwezera choipa chake posachedwa atamtsutsa munthu, ana a anthu atsimikizadi mitima yao kuchita zoipa.
Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m'dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova.
Efuremu iwe, ndidzakuchitira chiyani? Yuda iwe, ndikuchitire chiyani? Pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam'mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa.
umo anenamo, Lero ngati mudzamva mau ake, musaumitse mitima yanu, monga pa kupsetsa mtima.
musaumitse mitima yanu, monga m'kupsetsa mtimamo, monga muja tsiku la chiyesero m'chipululu,
Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalape kuti amchitire ulemu.
Ndipo ng'ombezo zinatsata njira yolunjika ku Betesemesi, zinali kuyenda mumseu, zilikulira; sizinapatukire ku dzanja lamanja, kapena kulamanzere; ndipo mafumu a Afilisti anazitsatira kufikira ku malire a Betesemesi.
Ndipo iwo anati, Ngati mulitumiza kwina likasa la Mulungu wa Israele, musalitumize lopanda kanthu; koma makamaka mulibweze ndi nsembe yopalamula, mukatero mudzachiritsidwa, ndi kudziwa chifukwa chake dzanja lake lili pa inu losachoka.
Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aejipito ndi Farao anaumitsa mitima yao? Kodi iwo sanalole anthuwo amuke, Iye atachita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka?
Ndipo muyang'anire, ngati likwera panjira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali.