Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Hoseya 6:4 - Buku Lopatulika

4 Efuremu iwe, ndidzakuchitira chiyani? Yuda iwe, ndikuchitire chiyani? Pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam'mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Efuremu iwe, ndidzakuchitira chiyani? Yuda iwe, ndikuchitire chiyani? Pakuti kukoma mtima kwako kukunga mtambo wam'mawa ndi ngati mame akuphawa mamawa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Koma Chauta akuti, “Inu Aefuremu, kodi ndikuchiteni chiyani? Nanga inu Ayuda, ndikuchiteni chiyani? Chikondi chanu chimazimirira ngati nkhungu yam'maŵa, chili ngati mame okamuka msanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Iwe Efereimu, kodi ndichite nawe chiyani? Kodi ndichite nawe chiyani, iwe Yuda? Chikondi chanu chili ngati nkhungu yammawa, ngati mame a mmamawa amene amakamuka msanga.

Onani mutuwo Koperani




Hoseya 6:4
19 Mawu Ofanana  

Ndipo zingakhale zonsezi Yuda mphwake wonyenga sanabwere kwa Ine ndi mtima wake wonse, koma monama, ati Yehova.


Koma Ine ndinati, Ndidzakuika iwe bwanji mwa ana, ndi kupatsa iwe dziko lokondweretsa, cholowa chabwino cha makamu a mitundu ya anthu? Ndipo ndinati mudzanditcha Ine, Atate wanga; osatembenuka kuleka kunditsata Ine.


Ndipo mwabwerera inu tsopano, ndi kuchita chimene chili cholungama pamaso panga, pakulalikira ufulu yense kwa mnzake; ndipo munapangana pangano pamaso panga m'nyumba imene itchedwa dzina langa;


Koma anthu awa ali ndi mtima woukirana ndi wopikisana; anapanduka nachoka.


Bwanji ndidzakhululukira iwe? Pamenepo ana ako andisiya Ine, nalumbira pa iyo yosati milungu; pamene ndinakhutitsa iwo, anachita chigololo, nasonkhana pamodzi m'nyumba za adama.


Kodi sindidzawalanga chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu woterewu?


Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzawasungunula, ndi kuwayesa, pakuti ndidzachitanji, chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu anga?


Ndidzakusiya bwanji, Efuremu? Ndidzakupereka bwanji, Israele? Ndidzakuyesa bwanji ngati Adima? Ndidzakuika bwanji ngati Zeboimu? Mtima wanga watembenuka m'kati mwanga, zachifundo zanga zilira zonse pamodzi.


Chifukwa chake adzakhala ngati mtambo wa m'mawa, ndi ngati mame akamuka mamawa, ngati mungu umene mphepo iuuluza kudwale, ndi ngati utsi wotuluka kukafwambira.


M'mene ndichiritsa Israele, mphulupulu ya Efuremu ivumbuluka, ndi zoipa za Samariya; pakuti achita bodza, ndipo mkhungu alowa m'nyumba, ndi gulu la mbala lilanda kubwalo.


ndipo alibe mizu mwa iye, koma akhala nthawi yaing'ono; ndipo pakudza nsautso kapena zunzo chifukwa cha mau, iye akhumudwa pomwepo.


Koma ana a Israele anaonjezanso kuchita choipa pamaso pa Yehova; pamenepo Yehova analimbitsa Egiloni mfumu ya Mowabu pa Israele, popeza anachita choipa pamaso pa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa