1 Samueli 6:9 - Buku Lopatulika9 Ndipo muyang'anire, ngati likwera panjira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20149 Ndipo muyang'anire, ngati likwera pa njira ya malire akeake ku Betesemesi, Iye anatichitira choipa ichi chachikulu; koma likapanda kutero, tidzadziwapo kuti dzanja limene linatikantha, silili lake; langotigwera tsokali. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa9 Tsono muziliyang'ana. Likamangopita kulondola kwao kwa Bokosilo mpaka kukafika ku Betesemesi, ndiye kutidi ndi Mulungu wa Aisraele amene adatidzetsera zovuta zazikuluzi. Koma zikapanda kutero, tidzadziŵa kuti sindiye amene adatizunza, zidangochitika mwatsoka.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero9 Koma muziliyangʼana. Ngati lilondola njira yopita kwawo kwa Bokosilo mpaka ku Beti-Semesi ndiye kuti amene watichita zoyipa zazikulu zoterezi ndi Mulungu wa Israeli. Koma ngati silitero, ife tidzadziwa kuti sanali Mulungu wa Israeli amene watizunza koma kuti zinangochitika mwatsoka.” Onani mutuwo |