Eksodo 8:29 - Buku Lopatulika29 Ndipo Mose anati, Onani, ndilikutuluka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza ichoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ake, ndi kwa anthu ake; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201429 Ndipo Mose anati, Onani, ndilikutuluka ine kwanu, ndidzapemba Yehova kuti mizaza ichoke mawa kwa Farao, ndi kwa anyamata ake, ndi kwa anthu ake; komatu, Farao asanyengenso ndi kukana kulola anthuwa amuke kukamphera nsembe Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa29 Apo Mose adati, “Malinga ndikachoka pano, ndikukapempha kwa Chauta, ndipo maŵa mizaza ikuchokani inu, nduna zanu ndiponso anthu anu. Koma musatinyengenso ndi kuŵaletsa anthu kupita kuti akapereke nsembe kwa Chauta.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero29 Mose anayankha kuti, “Ine ndikangochoka pano, ndikapemphera kwa Yehova ndipo mawa lomweli ntchentche zoluma zidzachoka kwa Farao, nduna zake pamodzi ndi anthu ake. Koma Farao, onetsetsani kuti musachitenso zachinyengo ndi kuwakaniza anthu kuti asakapereke nsembe kwa Yehova.” Onani mutuwo |