Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 8:32 - Buku Lopatulika

32 Koma Farao anaumitsa mtima wake nthawi yomweyonso, ndipo sanalole anthu amuke.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

32 Koma Farao anaumitsa mtima wake nthawi yomweyonso, ndipo sanalola anthu amuke.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

32 Koma ngakhale pa nthaŵi imeneyinso, Farao adakhala wokanikabe, ndipo sadalole kuti Aisraele apite.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

32 Koma nthawi imeneyinso Farao anawumitsa mtima wake ndipo sanalole kuti anthu atuluke.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 8:32
11 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Pakumuka iwe kubwerera kunka ku Ejipito, usamalire uchite zozizwa zonse ndaziika m'dzanja lako, pamaso pa Farao; koma Ine ndidzalimbitsa mtima wake kuti asadzalole anthu kupita.


Koma pamene Farao anaona kuti panali kupuma, anaumitsa mtima wake, osamvera iwo; monga adalankhula Yehova.


Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nachotsera Farao ndi anyamata ake ndi anthu ake mizazayo, sunatsale ndi umodzi wonse.


Pamenepo Farao anaitana Mose ndi Aroni, nati, Mundipembere Yehova, kuti andichotsere ine ndi anthu anga achulewo; ndipo ndidzalola anthu amuke, kuti amphere Yehova nsembe.


Ndipo Farao anatuma, taonani, sichidafe chingakhale chimodzi chomwe cha zoweta za Aisraele. Koma mtima wa Farao unauma, ndipo sanalole anthu amuke.


Yehova bwanji mwatisocheretsa kusiya njira zanu, ndi kuumitsa mitima yathu tisakuopeni? Bwerani, chifukwa cha atumiki anu, mafuko a cholowa chanu.


Koma kolingana ndi kuuma kwako, ndi mtima wako wosalapa, ulikudziunjikira wekha mkwiyo pa tsiku la mkwiyo ndi la kuvumbulutsa kuweruza kolungama kwa Mulungu;


Mulikuumitsiranji mitima yanu, monga Aejipito ndi Farao anaumitsa mitima yao? Kodi iwo sanalole anthuwo amuke, Iye atachita kodabwitsa pakati pao, ndipo anamuka?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa