Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 8:31 - Buku Lopatulika

31 Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nachotsera Farao ndi anyamata ake ndi anthu ake mizazayo, sunatsale ndi umodzi wonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Ndipo Yehova anachita monga mwa mau a Mose; nachotsera Farao ndi anyamata ake ndi anthu ake mizazayo, sunatsala ndi umodzi wonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Motero Chauta adachitadi monga momwe Mose adapemphera. Pomwepo mizaza idamchoka Farao ndi nduna zake ndi anthu ake omwe. Sudatsalepo ndi umodzi omwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Ndipo Yehova anachita zomwe Mose anapempha: Ntchentche zoluma zinachoka kwa Farao ndi nduna zake ndiponso kwa anthu ake. Palibe ngakhale imodzi yomwe inatsala.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 8:31
5 Mawu Ofanana  

Anapatuka onse; pamodzi anavunda mtima; palibe wakuchita bwino ndi mmodzi yense.


Pakuti ukapanda kulola anthu anga amuke, taona, ndidzatuma mizaza pa iwe, ndi pa anyamata ako, ndi pa anthu ako, ndi pa nyumba zako; ndipo nyumba za Aejipito zidzadzala nayo mizaza, ndi nthaka yomwe imene ikhalapo.


Ndipo Mose anatuluka kwa Farao, napemba Yehova.


Koma Farao anaumitsa mtima wake nthawi yomweyonso, ndipo sanalole anthu amuke.


Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m'dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa