Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 34:10 - Buku Lopatulika

Ndipo Iye anati, Taona, Ine ndichita pangano; ndidzachita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinachitike zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uliwonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pao adzaona ntchito ya Yehova, pakuti chinthu ndikuchitirachi nchoopsa.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Iye anati, Taona, Ine ndichita pangano; ndidzachita zozizwa pamaso pa anthu ako onse, sizinachitika zotere ku dziko lonse lapansi, kapena ku mtundu uliwonse wa anthu; ndipo anthu onse amene uli pakati pao adzaona ntchito ya Yehova, pakuti chinthu ndikuchitirachi nchoopsa.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pambuyo pake Chauta adati, “Ndidzachita nanu chipangano. Ndidzachita zozizwitsa zazikulu pamaso pa anthu ako onseŵa, zimene sizidachitikepo ndi kale lonse pa dziko lonse lapansi, pakati pa mitundu ina yonse. Anthu onse amene ali ndi iweŵa adzaona zimene Ine Chauta ndingathe kuchita, chifukwa zimene ndidzachita kudzera mwa iwe nzoopsa zedi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Choncho Yehova anati: “Ine ndikuchita nanu pangano. Ndidzachita zodabwitsa pamaso pa anthu onse zimene sizinachitikenso ndi mtundu wina uliwonse wa anthu pa dziko lonse lapansi. Anthu amene mudzakhala pakati pawo adzaona kuopsa kwa ntchito imene Ine Yehova ndidzakuchitireni.

Onani mutuwo



Eksodo 34:10
28 Mawu Ofanana  

Ndiponso mtundu uti wa padziko lapansi ufanana ndi anthu anu, ndiwo Israele, amene Mulungu anakadziombolera akhale anthu ake, ndi kuti limveke dzina lake, ndi kukuchitirani zinthu zazikulu ndi kuchitira dziko lanu zoopsa, pamaso pa anthu anu, amene munadziombolera kuwatulutsa ku dziko la Ejipito mwa amitundu ndi milungu yao?


zodabwitsa m'dziko la Hamu, zoopsa ku Nyanja Yofiira.


Amene yekha achita zodabwitsa zazikulu; pakuti chifundo chake nchosatha.


Ndipo adzanenera mphamvu za ntchito zanu zoopsa; ndi ukulu wanu ndidzaufotokozera.


Sanatero nao anthu a mtundu wina; ndipo za maweruzo ake, sanawadziwe. Aleluya.


Mudzatiyankha nazo zoopsa m'chilungamo, Mulungu wa chipulumutso chathu; ndinu chikhulupiriko cha malekezero onse a dziko lapansi, ndi cha iwo okhala kutali kunyanja.


Nenani kwa Mulungu, Ha, ntchito zanu nzoopsa nanga! Chifukwa cha mphamvu yanu yaikulu adani anu adzagonjera Inu.


Idzani, muone ntchito za Mulungu; zochitira Iye ana a anthu nzoopsa.


Inu Mulungu, ndinu woopsa m'malo oyera anu; Mulungu wa Israele ndiye amene apatsa anthu ake mphamvu ndi chilimbiko. Alemekezeke Mulungu.


Wolemekezeka Yehova Mulungu, Mulungu wa Israele, amene achita zodabwitsa yekhayo.


Iye adzadula mzimu wa akulu; akhala woopsa kwa mafumu a padziko lapansi.


Inu ndinu Mulungu wakuchita chodabwitsa; munazindikiritsa mphamvu yanu mwa mitundu ya anthu.


Anachita chodabwitsa pamaso pa makolo ao, m'dziko la Ejipito kuchidikha cha Zowani.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mau awa; pakuti monga mwa mau awa ndapangana ndi iwe ndi Israele.


Ndipo anakhala pomwepo ndi Yehova masiku makumi anai, usana ndi usiku; sanadye mkate kapena kumwa madzi. Ndipo analembera pa magomewo mau a panganolo, mau khumiwo.


Pamene Inu munachita zinthu zoopsa, zimene ife sitinayang'anira, Inu munatsika, mapiri anagwedezeka pamaso panu.


ndipo munatulutsa anthu anu Israele m'dziko la Ejipito ndi zizindikiro, ndi zodabwitsa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mantha ambiri;


Monga masiku a kutuluka kwako m'dziko la Ejipito ndidzamuonetsa zodabwitsa.


Iye ndiye lemekezo lanu, Iye ndiye Mulungu wanu, amene anachita nanu zazikulu ndi zoopsa izi, mudaziona m'maso mwanu.


Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova.


Pamenepo anakufotokozerani chipangano chake, chimene anakulamulirani kuchichita, ndiwo Mau Khumi; nawalemba pa magome awiri amiyala.


Pakuti ndinachita mantha chifukwa cha mkwiyo waukali, umene Yehova anakwiya nao pa inu kukuonongani. Koma Yehova anandimvera nthawi ijanso.


Ndipo anthu anafuula, naliza mphalasa ansembe; ndipo kunali, pamene anthu anamva kulira kwa mphalasa, anafuula anthu ndi mfuu yaikulu, niligwa linga pomwepo; nakwera anthu kulowa m'mzinda, yense kumaso kwake; nalanda mzindawo.