Eksodo 25:8 - Buku Lopatulika Ndipo andimangire malo opatulika; kuti ndikhale pakati pao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo andimangire malo opatulika; kuti ndikhale pakati pao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo andipangire chihema chopatulika kuti Ine ndidzakhale pakati pao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Iwo andipangire malo wopatulika, ndipo Ine ndidzakhala pakati pawo. |
Perekani tsono mtima ndi moyo wanu kufunafuna Yehova Mulungu wanu; ndipo nyamukani ndi kumanga malo opatulika a Yehova Mulungu, kuti abwere nalo likasa la chipangano la Yehova, ndi zipangizo zopatulika za Mulungu, kunyumba imene idzamangidwira dzina la Yehova.
Mudzawafikitsa, ndi kuwaoka paphiri la cholowa chanu, pamalo pamene munadzipangira mukhalepo, Yehova, malo oyera, amene manja anu, Ambuye, adakhazikika.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga, ndipo wakhala chipulumutso changa; ameneyo ndiye Mulungu wanga, ndidzamlemekeza; ndiye Mulungu wa kholo langa, ndidzamveketsa.
Ndipo adzadziwa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wao, amene ndinawatulutsa m'dziko la Ejipito, kuti ndikhale pakati pao. Ine ndine Yehova Mulungu wao.
Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.
Ndipo ndidzapangana nao pangano la mtendere, lidzakhala pangano losatha nao, ndipo ndidzawakhazika, ndi kuwachulukitsa, ndi kuika malo anga opatulika pakati pao kosatha.
Ndipo amitundu adzadziwa kuti Ine ndine Yehova wakupatula Israele, pokhala pakati pao malo anga opatulika kosatha.
Ndipo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, pano mpokhala mpando wachifumu wanga, mpoponda kumapazi anga, pomwe ndidzakhala pakati pa ana a Israele kosatha; ndi nyumba ya Israele siidzadetsanso dzina langa loyera, ngakhale iwo kapena mafumu ao, mwa chigololo chao, ndi mitembo ya mafumu ao pa misanje yao,
Ndipo Mose anaitana Misaele ndi Elizafani, ana a Uziyele, mbale wa atate wa Aroni, nanena nao, Senderani pafupi, nyamulani abale anu muwachotse pakhomo pa malo opatulika kunka nao kunja kwa chigono.
Asatuluke m'malo opatulika, kapena kuipsa malo opatulika a Mulungu wake; popeza korona wa mafuta odzoza wa Mulungu wake ali pa iye; Ine ndine Yehova.
ndipo wansembeyo aviike chala chake m'mwazimo, nawaze mwaziwo kasanu ndi kawiri pamaso pa Yehova chakuno cha nsalu yotchinga, ya malo opatulika.
Imba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndilinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova.
Atero Yehova: Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati pa Yerusalemu; ndi Yerusalemu adzatchedwa, Mzinda wa choonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, Phiri lopatulika.
muwatulutse amuna ndi akazi muwatulutsire kunja kwa chigono, kuti angadetse chigono chao, chimene ndikhala m'kati mwakemo.
Chihema cha umboni chinali ndi makolo athu m'chipululu, monga adalamula Iye wakulankhula ndi Mose, achipange ichi monga mwa chithunzicho adachiona.
Ndipo chiphatikizo chake nchanji ndi Kachisi wa Mulungu ndi wa mafano? Pakuti ife ndife Kachisi wa Mulungu wamoyo; monga Mulungu anati, Ndidzakhalitsa mwa iwo, ndipo ndidzayendayenda mwa iwo; ndipo ndidzakhala Mulungu wao, ndi iwo adzakhala anthu anga.
Pamenepo padzakhala malo amene Yehova Mulungu wanu adzasankha kukhalitsako dzina lake, kumeneko muzibwera nazo zonse ndikuuzanizi; nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zanu zophera, magawo anu onse a magawo khumi, ndi nsembe yokweza dzanja lanu, ndi zowinda zanu zosankhika zimene muzilonjezera Yehova.
koma Khristu monga mwana, wosunga nyumba yake; ndife nyumba yake, ngati tigwiritsa kulimbika mtima ndi kudzitamandira kwa chiyembekezocho, kuchigwira kufikira chitsiriziro.
Ndipo Finehasi, mwana wa Eleazara wansembe ananena ndi ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi ana a Manase, lero lino tidziwa kuti Yehova ali pakati pa ife, pakuti simunalakwira nacho Yehova; tsopano mwalanditsa ana a Israele m'dzanja la Yehova.
Ndipo ndinamva mau aakulu ochokera ku mpando wachifumu, ndi kunena Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nao, ndi iwo adzakhala anthu ake, ndi Mulungu yekha adzakhala nao, Mulungu wao;