Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Levitiko 21:12 - Buku Lopatulika

12 Asatuluke m'malo opatulika, kapena kuipsa malo opatulika a Mulungu wake; popeza korona wa mafuta odzoza wa Mulungu wake ali pa iye; Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Asatuluke m'malo opatulika, kapena kuipsa malo opatulika a Mulungu wake; popeza korona wa mafuta odzoza wa Mulungu wake ali pa iye; Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Asatuluke m'malo oyera kapena kuipitsa malo oyera a Mulungu wake, pakuti mafuta odzozera a Mulungu wake amene adamdzoza nawo ali pa iye. Ine ndine Chauta.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Asadzidetse potulukira kunja kwa malo opatulika popeza mafuta womupatula kukhala wansembe ali pamutu pake. Ine ndine Yehova.

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 21:12
9 Mawu Ofanana  

Ndipo upange golide waphanthiphanthi woona, ndi kulochapo, monga malochedwe a chosindikizira, Kupatulikira Yehova.


Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende;


Ndipo musatuluka pakhomo pa chihema chokomanako, kuti mungafe, pakuti mafuta odzoza a Yehova ali pa inu. Ndipo anachita monga mwa mau a Mose.


Ndipo adzitengere mkazi akali namwali.


Ndipo Mose anatengako mafuta odzoza, ndi mwazi unakhala paguwa la nsembewo, naziwaza pa Aroni, pa zovala zake, ndi pa ana ake aamuna, ndi pa zovala za ana ake aamuna omwe; napatula Aroni, ndi zovala zake, ndi ana ake aamuna, ndi zovala za ana ake aamuna omwe.


Masiku onse akudzipatulira kwa Yehova asayandikize mtembo.


za Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza Iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi mdierekezi, pakuti Mulungu anali pamodzi ndi Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa