Zekariya 2:10 - Buku Lopatulika10 Imba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndilinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Imba, nukondwere, mwana wamkazi wa Ziyoni; pakuti taonani, ndilinkudza, ndipo ndidzakhala pakati pako, ati Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 “Inu anthu a ku Ziyoni, imbani mokondwa, chifukwa ndikubwera, ndikudzakhala pakati panu,” akutero Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 “Iwe mwana wamkazi wa Ziyoni, fuwula ndipo sangalala. Pakuti taona ndikubwera, ndipo ndidzakhala pakati pako,” akutero Yehova. Onani mutuwo |
mudzamvekanso mau akukondwa ndi mau akusekera, mau a mkwati ndi mau a mkwatibwi, mau a iwo akuti, Myamikireni Yehova wa makamu, pakuti Yehova ndiye wabwino, chifundo chake nchosatha; ndi a iwo akutengera nsembe zoyamikira m'nyumba ya Yehova. Pakuti ndidzabweza undende wa dziko monga poyamba, ati Yehova.