Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 2:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Nthaŵi imeneyo anthu a mitundu yambiri adzabwera kwa Chauta, adzasanduka anthu ake, ndipo Iye adzakhala pakati panu. Apo mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse ndiye wandituma kwa inu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 “Nthawi imeneyo anthu a mitundu yambiri adzabwera kwa Yehova ndipo adzasanduka anthu anga. Ndidzakhala pakati pako ndipo iwe udzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse wandituma kwa iwe.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 2:11
36 Mawu Ofanana  

Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala.


Pakhale lamulo lomweli pa wobadwa m'dziko, ndi pa mlendo wakukhala pakati pa inu.


Atero Yehova, Ntchito ya Ejipito, ndi malonda a Kusi, ndi a Seba, amuna amsinkhu adzakugonjera, nadzakhala ako; nadzakutsata pambuyo m'maunyolo; adzakugonjera, nadzakugwira; adzakupembedza ndi kunena, Zoona Mulungu ali mwa iwe; ndipo palibenso wina, palibe Mulungu.


Idzani inu chifupi ndi Ine, imvani ichi; kuyambira pa chiyambi sindinanene m'tseri; chiyambire zimenezi, Ine ndilipo; ndipo tsopano Ambuye Mulungu wanditumiza Ine ndi mzimu wake.


Yehova wavula mkono wake woyera pamaso pa amitundu onse; ndi malekezero onse a dziko lapansi adzaona chipulumutso cha Mulungu wathu.


Chokani inu, chokani inu, tulukani ku Babiloni; musakhudze kanthu kodetsa; tulukani pakati pake, khalani okonzeka, inu amene munyamula zotengera za Yehova.


Ndipo ndidzaika chizindikiro pakati pao, ndipo ndidzatumiza onse amene apulumuka mwa iwo kwa amitundu, kwa Tarisisi, kwa Puti ndi kwa Aludi, okoka uta kwa Tubala ndi Yavani, kuzisumbu zakutali, amene sanamve mbiri yanga, ngakhale kuona ulemerero wanga; ndipo adzabukitsa ulemerero wanga pakati pa amitundu.


Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.


Thawani pakati pa Babiloni, tulukani m'dziko la Ababiloni, mukhale monga atonde patsogolo pa zoweta.


Ndipo pakuchitika ichi, pakuti chifikadi, pamenepo adzadziwa kuti panali mneneri pakati pao.


Ndipo amitundu ambiri adzamuka, nadzati, Tiyeni, tikwere kuphiri la Yehova, ndi kunyumba ya Mulungu wa Yakobo; kuti Iye atiphunzitse njira zake, ndipo tidzayenda m'mabande ake; pakuti ku Ziyoni kudzatuluka chilamulo, ndi ku Yerusalemu mau a Yehova.


Chifukwa chake atero Yehova: Ndabwera kudza ku Yerusalemu ndi zachifundo; nyumba yanga idzamangidwamo, atero Yehova wa makamu, ndipo adzayesa Yerusalemu ndi chingwe.


Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pake, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwake.


Tsiku lomwelo, ati Yehova wa makamu, mudzaitanizana yense mnansi wake patsinde pa mpesa ndi patsinde pa mkuyu.


Atero Yehova: Ndabwerera kudza ku Ziyoni, ndidzakhala pakati pa Yerusalemu; ndi Yerusalemu adzatchedwa, Mzinda wa choonadi; ndi phiri la Yehova wa makamu, Phiri lopatulika.


ndipo ndidzabwera nao, nadzakhala m'kati mwa Yerusalemu; ndipo iwo adzakhala anthu anga, nanenanso ndidzakhala Mulungu wao, m'choonadi ndi m'chilungamo.


Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.


kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israele.


kuti onse akakhale amodzi, monga Inu Atate mwa Ine, ndi Ine mwa Inu, kuti iwonso akakhale mwa Ife: kuti dziko lapansi likakhulupirire kuti Inu munandituma Ine.


Ine mwa iwo, ndi Inu mwa Ine, kuti akhale angwiro mwa mmodzi; kuti dziko lapansi lizindikire kuti Inu munandituma Ine, nimunawakonda iwo, monga momwe munakonda Ine.


Atate wolungama, dziko lapansi silinadziwe Inu, koma Ine ndinadziwa Inu; ndipo iwo anazindikira kuti munandituma Ine;


Potero, dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwa amitundu; iwonso adzamva.


Ndipo mngelo wachisanu ndi chiwiri anaomba lipenga, ndipo panakhala mau aakulu mu Mwamba, ndi kunena, Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu, ndi wa Khristu wake: ndipo adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa