Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Zekariya 2:9 - Buku Lopatulika

9 Pakuti, taonani, ndidzawayambasira dzanja langa, ndipo adzakhala zofunkha za iwo amene anawatumikira; ndipo mudzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Pakuti, taonani, ndidzawayambasira dzanja langa, ndipo adzakhala zofunkha za iwo amene anawatumikira; ndipo mudzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 “Ine Chauta ndidzaŵamenya anthuwo ndi dzanja langa, ndipo amene anali akapolo ao, ndiwo amene adzaŵalande chuma chao.” Pamenepo mudzadziŵa kuti Chauta Wamphamvuzonse ndiye wandituma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ndithu Ine ndidzawamenya anthuwo ndi dzanja langa ndipo amene anali akapolo awo ndiye adzawalande zinthu. Pamenepo mudzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse ndiye wandituma.

Onani mutuwo Koperani




Zekariya 2:9
30 Mawu Ofanana  

Lero lomwe adzaima pa Nobu; agwedezera dzanja lake paphiri la mwana wamkazi wa Ziyoni, phiri la Yerusalemu.


Ndipo Yehova adzaononga ndithu bondo la nyanja ya Ejipito; ndipo ndi mphepo yake yopsereza adzagwedeza dzanja lake pa Mtsinje, ndipo adzaimenya ikhale mphaluka zisanu ndi ziwiri, nadzaolotsa anthu pansi pouma.


Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.


Kwezani mbendera paphiri loti see, kwezani mau kwa iwo, kodolani kuti alowe m'zipata za akulu.


Ndipo mitundu ya anthu idzawatenga, ndi kuwafikitsa kumalo a kwao; ndipo a nyumba ya Israele adzakhala nao amitunduwo m'dziko la Yehova, ndi kuwayesa atumiki ndi adzakazi, ndipo amitunduwo adzatengedwa ndende, ndi amenewo anali ndende zao; ndipo Aisraele adzalamulira owavuta.


Tsiku limenelo Ejipito adzanga akazi; ndipo adzanthunthumira ndi kuopa, chifukwa cha kugwedeza kwa dzanja la Yehova wa makamu, limene Iye agwedeza pamwamba pake.


Tsiku limenelo adzaimba nyimbo imeneyi m'dziko la Yuda, Ife tili ndi mzinda wolimba; Iye adzaika chipulumutso chikhale machemba ndi malinga.


Tsoka kwa iwe amene usakaza, chinkana sunasakazidwe; nupangira chiwembu, chinkana sanakupangire iwe chiwembu! Utatha kusakaza, iwe udzasakazidwa; ndipo utatha kupangira chiwembu, iwo adzakupangira iwe chiwembu.


Koma pamenepo Yehova adzakhala ndi ife mu ulemerero, malo a nyanja zachitando ndi mitsinje; m'menemo ngalawa sizidzayenda ndi ngombo, ngakhale zombo zazikulu sizidzapita pamenepo.


Zingwe zako za ngalawa zamasulidwa; sizinathe kulimbitsa patsinde pa mlongoti wake, sizinathe kufutukula matanga; pamenepo ndipo cholanda chachikulu, chofunkha chinagawanidwa; wopunduka nafumfula.


Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse paphiri la Ziyoni, ndi pa misonkhano yake, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; chifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa chophimba.


Idzani inu chifupi ndi Ine, imvani ichi; kuyambira pa chiyambi sindinanene m'tseri; chiyambire zimenezi, Ine ndilipo; ndipo tsopano Ambuye Mulungu wanditumiza Ine ndi mzimu wake.


Chiwawa sichidzamvekanso m'dziko mwako, kupululutsa pena kupasula m'malire ako; koma udzatcha malinga ako Chipulumutso, ndi zipata zako Matamando.


Dzuwa silidzakhalanso kuunika kwako usana, ngakhale mwezi sudzakuunikiranso kuti kuyere; koma Yehova adzakhala kwa iwe kuunika kosatha, ndi Mulungu wako adzakhala ulemerero wako.


Ndipo amitundu onse adzamtumikira iye, ndi mwana wake, ndi mdzukulu wake, mpaka yafika nthawi ya dziko lake; ndipo amitundu ambiri ndi mafumu aakulu adzamuyesa iye mtumiki wao.


Mneneri amene anenera za mtendere, pamene mau a mneneri adzachitidwa, pamenepo mneneri adzadziwika, kuti Yehova anamtuma ndithu.


Taonani, mau a kulira kwa mwana wamkazi wa anthu anga ochokera kudziko lakutali: Kodi mu Ziyoni mulibe Yehova? Kodi mulibe mfumu yake? Chifukwa chanji andiputa Ine ndi mafano ao osema, ndi zachabe zachilendo?


osatenga nkhuni kuthengo, kapena kuzitema kunkhalango; popeza adzasonkha moto ndi zidazo; nadzafunkha iwo amene anawafunkha, ndi kulanda zao za iwo adalanda zaozo, ati Ambuye Yehova.


Ndipo mudzadziwa kuti Ine ndili pakati pa Israele, ndi kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, palibe wina; ndi anthu anga sadzachita manyazi nthawi zonse.


Pakuti chiwawa chidachitikira Lebanoni chidzakukuta, ndi chionongeko cha nyama chidzakuopsa; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitidwira dziko, mzinda, ndi onse okhalamo.


Popeza iwe wafunkha amitundu ambiri, otsala onse a mitundu ya anthu adzakufunkha iwe; chifukwa cha mwazi wa anthu, ndi chiwawa chochitikira dziko, mzinda, ndi onse okhalamo.


Chifukwa chake, pali moyo wanga, ati Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele, Zedi Mowabu adzakhala ngati Sodomu, ndi ana a Amoni ngati Gomora, pochuluka khwisa ndi maenje a mchere, ndi bwinja losatha; otsala a anthu anga adzalanda zao, ndi otsala a mtundu wa anthu anga adzawalandira akhale cholowa chao.


Yehova wachotsa maweruzo ako, anataya kunja mdani wako; mfumu ya Israele, Yehova, ali pakati pako, sudzaopanso choipa.


Ndipo amitundu ambiri adzaphatikidwa kwa Yehova tsiku ilo, nadzakhala anthu anga; ndipo ndidzakhala pakati pako, ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa iwe.


Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lake.


Manja a Zerubabele anaika maziko a nyumba iyi, manja ake omwe adzaitsiriza; ndipo udzadziwa kuti Yehova wa makamu anandituma kwa inu.


Ndipo iwo akukhala kutali adzafika, nadzamanga ku Kachisi wa Yehova, ndipo inu mudzadziwa kuti Yehova wa makamu ananditumiza kwa inu. Ndipo ichi chidzachitika ngati mudzamvera mwachangu mau a Yehova Mulungu wanu.


Yehova wa makamu adzawatchinjiriza; ndipo adzadza, nadzapondereza miyala yoponyera; ndipo adzamva, nadzachita phokoso ngati avinyo; ndipo adzadzazidwa ngati mbale, ngati ngodya za guwa la nsembe.


Kuyambira tsopano ndinena kwa inu, chisadachitike, kuti pamene chitachitika, mukakhulupirire kuti ndine amene.


Koma zinthu izi ndalankhula ndi inu kuti ikadza nthawi yao, mukakumbukire kuti ndinakuuzani. Koma izi sindinanene kwa inu kuyambira pachiyambi, chifukwa ndinali pamodzi ndi inu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa