Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Levitiko 10:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo Mose anaitana Misaele ndi Elizafani, ana a Uziyele, mbale wa atate wa Aroni, nanena nao, Senderani pafupi, nyamulani abale anu muwachotse pakhomo pa malo opatulika kunka nao kunja kwa chigono.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo Mose anaitana Misaele ndi Elizafani, ana a Uziyele, mbale wa atate wa Aroni, nanena nao, Senderani pafupi, nyamulani abale anu muwachotse pakhomo pa malo opatulika kunka nao kunja kwa chigono.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mose adaitana Misaele ndi Elizafani, ana a Uziyele, bambo wamng'ono wa Aroni, naŵauza kuti, “Senderani pafupi, achotseni abale anuŵa pa malo oyera ndipo muŵatulutsire kunja kwa mahema.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Mose anayitana Misaeli ndi Elizafani, ana a Uzieli, abambo angʼono a Aaroni, ndipo anawawuza kuti, “Bwerani kuno mudzachotse abale anuwa pa malo wopatulika ndi kuwatulutsira kunja kwa msasa.”

Onani mutuwo Koperani




Levitiko 10:4
10 Mawu Ofanana  

Ndi ana a Kohati: Amuramu, Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele.


Ndipo Mose akatenga chihemacho nachimanga kunja kwa chigono, kutali kwa chigono; nachitcha, Chihema chokomanako. Ndipo kunakhala kuti yense wakufuna Yehova anatuluka kunka ku chihema chokomanako kunja kwa chigono.


Ndi ana aamuna a Kohati ndiwo: Amuramu ndi Izihara, ndi Hebroni, ndi Uziyele; ndipo zaka za moyo wa Kohati ndizo zana limodzi ndi makumi atatu ndi kudza zitatu.


Ndi ana aamuna a Uziyele ndiwo: Misaele, ndi Elizafani, ndi Sitiri.


Ndi ana a Kohati monga mwa mabanja ao: Amuramu ndi Izihara, Hebroni ndi Uziyele.


Ndipo kalonga wa nyumba ya makolo ao ya mabanja a Akohati ndiye Elizafani mwana wa Uziyele.


Ndipo pamene anayandikira kuchipata cha mzindawo, onani, anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye; ndipo anthu ambiri amumzinda anali pamodzi naye.


Ndipo ananyamuka anyamata, namkulunga, namnyamula, natuluka naye, namuika.


Ndipo anamuika Stefano anthu opembedza, namlira maliro aakulu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa