Levitiko 10:3 - Buku Lopatulika3 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo Mose anati kwa Aroni, Ichi ndi chimene Yehova ananena, ndi kuti, Mwa iwo akundiyandikiza ndipatulidwa Ine, ndi pamaso pa anthu onse ndilemekezedwa. Ndipo Aroni anakhala chete. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Apo Mose adauza Aroni kuti, “Pajatu Chauta adanena kuti, ‘Ndidzaonetsa ulemerero wanga kwa onse amene ali pafupi ndi Ine, ndipo ndidzalemekezedwa pamaso pa anthu onse.’ ” Koma Aroni adakhala chete osalankhula. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Pamenepo Mose anawuza Aaroni kuti, “Pajatu Yehova ananena kuti, “ ‘Kwa iwo amene amandiyandikira ndidzaonetsa ulemerero wanga; pamaso pa anthu onse ndidzalemekezedwa.’ ” Aaroni anakhala chete wosayankhula. Onani mutuwo |
Pamenepo anati kwa ine, Zipinda za kumpoto, ndi zipinda za kumwera, zili chakuno cha mpatawo, ndizo zipinda zopatulika, kumene ansembe okhala pafupi pa Yehova azidyera zinthu zopatulika kwambiri; kumeneko aziika zopatulika kwambiri, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yauchimo, ndi nsembe yopalamula; pakuti malowo ndi opatulika.