Eksodo 17:9 - Buku Lopatulika Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nutuluke kuyambana naye Amaleke; mawa ndidzaima pamwamba pa chitunda, ndi ndodo ya Mulungu m'dzanja langa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nutuluke kuyambana naye Amaleke; mawa ndidzaima pamwamba pa chitunda, ndi ndodo ya Mulungu m'dzanja langa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mose adauza Yoswa kuti, “Tisankhulireko amuna ena, maŵa mupite kukamenyana nawo nkhondo Aamaleke. Ine ndidzaimirira pamwamba pa phiri, nditagwira ndodo adandipatsa Mulungu ija.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mose anati kwa Yoswa, “Sankha amuna amphamvu ndipo upite ukamenyane ndi Amaleki. Mawa ndidzayima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu.” |
Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;
Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kunka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoke m'chihemamo.
Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, nawakweza pabulu, nabwerera kunka ku dziko la Ejipito; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lake.
Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha nati, Mose, mfumu yanga, aletseni.
Awa ndi maina a amunawo Mose anawatumira azonde dziko. Ndipo Mose anamutcha Hoseya mwana wa Nuni Yoswa.
Ndipo Yehova anati kwa Mose, Utenge Yoswa mwana wa Nuni, ndiye munthu mwa iye muli mzimu, nuike dzanja lako pa iye;
Chimenenso makolo athu akudza m'mbuyo, analowa nacho ndi Yoswa polandira iwo zao za amitundu, amene Mulungu anawaingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide;
Ndipo anadza Mose nanena mau onse a nyimbo iyi m'makutu mwa anthu, iye, ndi Yoswa mwana wa Nuni.
Pamenepo Yehova anati kwa Yoswa, Tambasula nthungoyo ili m'dzanja lako iloze ku Ai, pakuti ndidzaupereka m'dzanja lako. Ndipo Yoswa anatambasula nthungoyo inali m'dzanja lake kuloza mzinda.
Pamenepo anauka Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo, kuti akwere ku Ai; ndipo Yoswa anasankha amuna zikwi makumi atatu, ndiwo ngwazi, nawatumiza apite usiku,