Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 13:16 - Buku Lopatulika

16 Awa ndi maina a amunawo Mose anawatumira azonde dziko. Ndipo Mose anamutcha Hoseya mwana wa Nuni Yoswa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Awa ndi maina a amunawo Mose anawatumira azonde dziko. Ndipo Mose anamutcha Hoseya mwana wa Nuni Yoswa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Ameneŵa ndiwo maina a anthu amene Mose adaŵatuma kukazonda dziko. Ndipo Hoseya mwana wa Nuni, Mose adamutcha dzina loti Yoswa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Amenewa ndiwo mayina a anthu amene Mose anawatuma kukazonda dzikolo. (Hoseya mwana wa Nuni, Mose anamupatsa dzina loti Yoswa).

Onani mutuwo Koperani




Numeri 13:16
14 Mawu Ofanana  

Nuni mwana wake, Yoswa mwana wake.


Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nutuluke kuyambana naye Amaleke; mawa ndidzaima pamwamba pa chitunda, ndi ndodo ya Mulungu m'dzanja langa.


Mau a Yehova amene anadza kwa Hoseya mwana wa Beeri masiku a Uziya, Yotamu, Ahazi, ndi Hezekiya, mafumu a Yuda, ndi masiku a Yerobowamu mwana wa Yowasi mfumu ya Israele.


Wa fuko la Gadi, Geuwele mwana wa Maki.


Udzitumire amuna, kuti azonde dziko la Kanani, limene ndilikupatsa ana a Israele; utumize munthu mmodzi wa fuko lililonse la makolo ao, yense kalonga pakati pa anzake.


Wa fuko la Efuremu, Hoseya mwana wa Nuni.


simudzalowa inu m'dzikolo, ndinakwezapo dzanja langa kukukhalitsani m'mwemo, koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni ndiwo.


Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, ndi Kalebe mwana wa Yefune, ndiwo a iwo aja adazonda dzikolo, anang'amba zovala zao;


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Utenge Yoswa mwana wa Nuni, ndiye munthu mwa iye muli mzimu, nuike dzanja lako pa iye;


Chimenenso makolo athu akudza m'mbuyo, analowa nacho ndi Yoswa polandira iwo zao za amitundu, amene Mulungu anawaingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide;


Monga atinso mwa Hoseya, Amene sanakhale anthu anga, ndidzawatcha anthu anga; ndi iye amene sanali wokondedwa, wokondedwa.


Ndipo anadza Mose nanena mau onse a nyimbo iyi m'makutu mwa anthu, iye, ndi Yoswa mwana wa Nuni.


Pakuti ngati Yoswa akadawapumitsa iwo, sakadalankhula m'tsogolomo za tsiku lina.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa