Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 17:13 - Buku Lopatulika

13 Ndipo Yoswa anathyola Amaleke ndi anthu ake ndi ukali wa lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

13 Ndipo Yoswa anathyola Amaleke ndi anthu ake ndi ku ukali kwa lupanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

13 Ndipo Yoswa adagonjetseratu kwathunthu Aamalekewo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

13 Kotero Yoswa anagonjetsa asilikali ankhondo a Amaleki ndi lupanga.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 17:13
9 Mawu Ofanana  

Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ake, wina mbali ina, wina mbali ina; ndi manja ake analimbika kufikira litalowa dzuwa.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m'buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleke pansi pa thambo.


Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira.


Ndipo Yoswa anagwira Makeda tsiku lomwe lija ndi kuukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yake yomwe; anawaononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, nachitira mfumu ya ku Makeda monga anachitira mfumu ya ku Yeriko.


napereka Yehova Lakisi m'dzanja la Israele, ndipo anaulanda tsiku lachiwiri, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi amoyo onse anali m'mwemo monga mwa zonse anachitira Libina.


naulanda, naukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yake ndi midzi yake yonse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, monga mwa zonse anachitira Egiloni; koma anauononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo.


Ndipo Yoswa anagwira mafumu awa onse ndi dziko lao nthawi yomweyi; chifukwa Yehova Mulungu wa Israele anathirira Israele nkhondo.


Ndipo Yoswa analanda mizinda yonse ya mafumu awa, ndi mafumu ao omwe nawakantha ndi lupanga lakuthwa, nawaononga konse; monga Mose mtumiki wa Yehova adalamulira.


Popeza Yoswa sanabweze dzanja lake limene anatambasula nalo nthungo, mpaka ataononga konse nzika zonse za ku Ai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa