Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 17:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m'buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleke pansi pa thambo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo Yehova anati kwa Mose, Lembera ichi m'buku, chikhale chikumbutso, nuchimvetse Yoswa; kuti ndidzafafaniza konse chikumbukiro cha Amaleke pansi pa thambo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 Tsono Chauta adauza Mose kuti, “Zimenezi muzilembe m'buku kuti zidzakumbukike, ndipo munene pamaso pa Yoswa kuti Aamalekewo adzafafanizika kwathunthu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 Kenaka Yehova anati kwa Mose, “Lemba izi mʼbuku kuti zidzakumbukirike ndipo uwonetsetse kuti Yoswa amve zimenezi, chifukwa Ine ndidzafafaniziratu Amaleki pa dziko lapansi, kotero kuti palibe amene adzawakumbukire.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 17:14
30 Mawu Ofanana  

Ndipo kunali atamwalira Saulo, pamene Davide anabwera atawapha Aamaleke, ndipo Davide atakhala ku Zikilagi masiku awiri;


za Aaramu, za Amowabu, za ana a Amoni, za Afilisti, za Amaleke, ndi zofunkha za Hadadezere, mwana wa Rehobu mfumu ya ku Zoba.


Ndipo ena a iwowa a ana a Simeoni, amuna mazana asanu, ananka kuphiri la Seiri; akuwatsogolera ndiwo Pelatiya, ndi Neariya, ndi Refaya, ndi Uziyele; ana a Isi.


Nakantha otsala a Aamaleke adapulumukawo, nakhala komweko mpaka lero lino.


kodi tidzabwereza kuphwanya malamulo anu, ndi kukwatirana nayo mitundu ya anthu ochita zonyansa izi? Simudzakwiya nafe kodi mpaka mwatitha, ndi kuti pasakhale otsala kapena akupulumuka?


Chikumbukiro chake chidzatayika m'dziko, ndipo adzasowa dzina kukhwalala.


Ha! Akadalembedwa mau anga! Ha! Akadalembedwa m'buku!


Adaniwo atha psiti, apululuka nthawi zonse; ndipo mizindayo mwaipasula, chikumbukiro chao pamodzi chatha.


Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.


Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chikumbutso pakati pamaso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.


Ndipo Yoswa anathyola Amaleke ndi anthu ake ndi ukali wa lupanga.


Ndipo Mose analembera mau onse a Yehova, nalawira kuuka mamawa, namanga guwa la nsembe patsinde paphiri, ndi zoimiritsa khumi ndi ziwiri, kwa mafuko khumi ndi awiri a Israele.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Iye amene wandichimwira, ndifafaniza yemweyo kumchotsa m'buku langa.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Ulembere mau awa; pakuti monga mwa mau awa ndapangana ndi iwe ndi Israele.


Amayesa wolungama wodala pomkumbukira; koma dzina la oipa lidzavunda.


Atero Yehova, Mulungu wa Israele, kuti, Lemba m'buku mau onse amene ndanena kwa iwe.


Tenga buku lampukutu, nulembe m'menemo mau onse ndanena kwa iwe akunenera Israele, ndi akunenera Yuda, ndi akunenera amitundu onse kuyambira tsiku ndinanena kwa iwe, kuyambira masiku a Yosiya, mpaka lero.


Ndipo anayang'ana ku Amaleke, nanena fanizo lake, nati, Amaleke ndiye woyamba wa amitundu; koma chitsiriziro chake, adzaonongeka ku nthawi zonse.


Ndipo Mose analembera matulukidwe ao monga mwa maulendo ao, monga mwa mau a Yehova; ndipo maulendo ao ndi awa monga mwa matulukidwe ao.


Ndipo Mose analembera chilamulo ichi, nachipereka kwa ansembe, ana a Levi, akunyamula likasa la chipangano la Yehova, ndi kwa akulu onse a Israele.


Munene nao, Chifukwa madzi a Yordani anadulidwa patsogolo pa likasa la chipangano cha Yehova; muja lidaoloka Yordani, madzi a Yordani anadulidwa; ndipo miyala iyi idzakhala chikumbutso cha ana a Israele chikhalire.


Ndipo Yehova anakutumani ulendo, kuti, Muka, nuononge konsekonse Aamaleke akuchita zoipawo, nuponyane nao kufikira utawatha.


Ndipo kunali, pakufika Davide ndi anthu ake ku Zikilagi tsiku lachitatu, Aamaleke adaponya nkhondo yovumbulukira kumwera, ndi ku Zikilagi, nathyola Zikilagi nautentha ndi moto;


Ndipo Davide anawakantha kuyambira madzulo kufikira usiku wa mawa wake; ndipo panalibe munthu mmodzi wa iwowa anapulumuka, koma anyamata mazana anai oberekeka pa ngamira, nathawa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa