Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 17:12 - Buku Lopatulika

12 Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ake, wina mbali ina, wina mbali ina; ndi manja ake analimbika kufikira litalowa dzuwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ake, wina mbali ina, wina mbali ina; ndi manja ake analimbika kufikira litalowa dzuwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Tsono manja a Mose atatopa, Aroni pamodzi ndi Huri uja adatenga mwala namkhazikira Mose kuti akhalepo. Aŵiriwo adakhala wina uku wina uku, atagwirira manja a Mose aja. Adaŵagwirira ndithu mpaka dzuŵa kuloŵa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Manja a Mose atatopa, Aaroni ndi Huri anatenga mwala ndi kuyika pansi ndipo Mose anakhalapo. Aaroni ndi Huri anagwirizitsa manja a Mose wina mbali ina winanso mbali ina. Choncho manja a Mose analimba mpaka kulowa kwa dzuwa.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 17:12
15 Mawu Ofanana  

Sololani nthungo, ndipo muwatsekerezere kunjira akundilondola. Nenani ndi moyo wanga, Chipulumutso chako ndine.


Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lake Israele anapambana; koma pamene anatsitsa dzanja lake Amaleke anapambana.


Ndipo Yoswa anathyola Amaleke ndi anthu ake ndi ukali wa lupanga.


Ndipo anati kwa akulu, Tilindeni kuno kufikira tidzabwera kwa inu; ndipo taonani, Aroni ndi Huri ali nanu; munthu akakhala ndi mlandu abwere kwa iwowa.


Limbitsani manja opanda mphamvu, ndi kulimbitsa maondo a gwedegwede.


pothandizana inunso ndi pemphero lanu la kwa ife; kuti pa mphatso ya kwa ife yodzera kwa anthu ambiri, payamikike ndi anthu ambiri chifukwa cha ife.


mwa pemphero lonse ndi pembedzero mupemphere nthawi yonse mwa Mzimu, ndipo pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse,


Pakuti ndidziwa kuti ichi chidzandichitira ine chipulumutso, mwa pembedzero lanu ndi mwa kundipatsako kwa Mzimu wa Yesu Khristu;


Chitani khama m'kupemphera, nimudikire momwemo ndi chiyamiko;


Abale, tipempherereni ife.


Mwa ichi limbitsani manja ogooka, ndi maondo olobodoka;


Koma apemphe ndi chikhulupiriro, wosakayika konse; pakuti wokayikayo afanana ndi funde la nyanja lotengeka ndi mphepo ndi kuwinduka nayo.


Popeza Yoswa sanabweze dzanja lake limene anatambasula nalo nthungo, mpaka ataononga konse nzika zonse za ku Ai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa