Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 17:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lake Israele anapambana; koma pamene anatsitsa dzanja lake Amaleke anapambana.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo kunakhala, pamene Mose anakweza dzanja lake Israele analakika; koma pamene anatsitsa dzanja lake Amaleke analakika.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Mose ankati akakweza manja ake, Aisraele ankapambana pa nkhondoyo, koma akatsitsa pansi manja, Aamaleke ankapambana.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Mose ankati akakweza manja ake, Aisraeli amapambana, koma akatsitsa manja akewo Amaleki amapambana.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 17:11
8 Mawu Ofanana  

Pakuti uta wanga, ndipo lupanga langa silingandipulumutse.


Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine. Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.


Ndipo Yoswa anachita monga Mose adanena naye, nayambana ndi Amaleke; ndipo Mose, ndi Aroni, ndi Huri anakwera pamwamba pa chitunda.


Koma manja a Mose analema; ndipo anatenga mwala, nauika pansi pa iye, nakhala pamenepo; ndipo Aroni ndi Huri anagwiriziza manja ake, wina mbali ina, wina mbali ina; ndi manja ake analimbika kufikira litalowa dzuwa.


Ndipo anawanenera fanizo lakuti ayenera iwo kupemphera nthawi zonse, osafooka mtima;


Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.


Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake.


Popeza Yoswa sanabweze dzanja lake limene anatambasula nalo nthungo, mpaka ataononga konse nzika zonse za ku Ai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa