Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 7:45 - Buku Lopatulika

45 Chimenenso makolo athu akudza m'mbuyo, analowa nacho ndi Yoswa polandira iwo zao za amitundu, amene Mulungu anawaingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

45 Chimenenso makolo athu akudza m'mbuyo, analowa nacho ndi Yoswa polandira iwo zao za amitundu, amene Mulungu anawaingitsa pamaso pa makolo athu, kufikira masiku a Davide;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

45 Chihemacho chimene makolo athu adachilandira kwa makolo ao aja, adabwera nacho kuno Yoswa akuŵatsogolera pamene adalanda dziko kwa mitundu ya anthu imene Mulungu adaipitikitsa iwo akufika. Chidakhala pakati pao mpaka nthaŵi ya Davide.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

45 Makolo athu, atayilandira Tentiyo, anabwera nayo motsogozedwa ndi Yoswa pamene analanda dziko la mitundu imene Mulungu anayipirikitsa pamaso pawo. Tentiyo inakhala mʼdzikomo mpaka nthawi ya Davide,

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 7:45
20 Mawu Ofanana  

Ndipo anatenga likasa la Yehova, ndi chihema chokomanako, ndi zipangizo zonse zopatulika, zinali m'chihemamo, inde zimenezi anazitenga ansembe ndi Alevi.


ndi Zadoki wansembe, ndi abale ake ansembe, ku chihema cha Yehova, pa msanje unali ku Gibiyoni;


Pakuti chihema cha Yehova amene Mose anapanga m'chipululu, ndi guwa la nsembe yopsereza, zinali pa msanje wa ku Gibiyoni nthawi yomweyi.


Nuni mwana wake, Yoswa mwana wake.


Nalowa anawo, nalandira dzikoli likhale laolao, ndipo munagonjetsa pamaso pao okhala m'dziko, ndiwo Akanani, ndi kuwapereka m'dzanja mwao, pamodzi ndi mafumu ao, ndi mitundu ya anthu ya m'dziko, kuti achite nao chifuniro chao.


Inu munapirikitsa amitundu ndi dzanja lanu, koma iwowa munawaoka; munasautsa mitundu ya anthu, ndipo munawaingitsa.


Ndipo anapirikitsa amitundu pamaso pao, nawagawira cholowa chao, ndi muyeso, nakhalitsa mafuko a Israele m'mahema mwao.


Mudatenga mpesa kuchokera ku Ejipito, munapirikitsa amitundu ndi kuuoka uwu.


Ndipo m'mene adaononga mitundu ya anthu isanu ndi iwiri mu Kanani, anawapatsa cholowa dziko lao, monga zaka mazana anai kudza makumi asanu;


Kwera m'phiri muno mwa Abarimu, phiri la Nebo, lokhala m'dziko la Mowabu, popenyana ndi Yeriko; nupenye dziko la Kanani, limene ndipereka kwa ana a Israele likhale laolao;


Pakuti ngati Yoswa akadawapumitsa iwo, sakadalankhula m'tsogolomo za tsiku lina.


Ndipo msonkhano wonse wa ana a Israele unasonkhana ku Silo, nuutsa komweko chihema chokomanako; ndipo dziko linawagonjera.


Pakuti Yehova anaingitsa pamaso panu mitundu yaikulu ndi yamphamvu; koma inu, palibe munthu anaima pamaso panu mpaka lero lino.


ndipo Yehova anaingitsa pamaso pathu anthu awa onse, ngakhale Aamori okhala m'dzikomo; chifukwa chake ifenso tidzatumikira Yehova, pakuti ndiye Mulungu wathu.


Motero anadziikira fano losema la Mika, limene adalipanga, masiku onse okhala nyumba ya Mulungu ku Silo.


Chifukwa chake anatumiza ku Silo kuti akatenge kumeneko likasalo la chipangano la Yehova wa makamu, wokhala pakati pa akerubi; ndipo ana awiriwo a Eli, Hofeni ndi Finehasi anali komweko ndi likasa la chipangano la Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa