Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 33:11 - Buku Lopatulika

11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kunka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoke m'chihemamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Ndipo Yehova ananena ndi Mose kopenyana maso, monga munthu alankhula ndi bwenzi lake. Ndipo anabwerera kunka kuchigono; koma mtumiki wake Yoswa mwana wa Nuni, ndiye mnyamata msinkhu wake, sanachoke m'chihemamo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Choncho Chauta ankalankhula ndi Mose pamasompamaso, monga momwe munthu amalankhulira ndi bwenzi lake. Tsono pambuyo pake Mose ankabwerera kumahema komweko. Koma mnyamata wina, dzina lake Yoswa, mwana wa Nuni, amene anali mtumiki wa Mose, sankachoka kuchihemako.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Yehova amayankhula ndi Mose maso ndi maso ngati mmene munthu amayankhulira ndi bwenzi lake. Kenaka Mose amabwerera ku msasa koma womuthandiza wake, Yoswa, mwana wa Nuni samachoka pa tentiyo.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 33:11
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Yakobo anatcha dzina la malo amenewo, Penuwele: chifukwa ndaonana ndi Mulungu nkhope ndi nkhope, ndipo wapulumuka moyo wanga.


Sindinu Mulungu wathu, amene munainga nzika za m'dziko muno pamaso pa ana anu Israele, ndi kulininkha kwa mbeu ya Abrahamu bwenzi lanu kosatha?


Ha? Munthu akadapembedzera mnzake kwa Mulungu, monga munthu apembedzera mnansi wake!


Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nutuluke kuyambana naye Amaleke; mawa ndidzaima pamwamba pa chitunda, ndi ndodo ya Mulungu m'dzanja langa.


Ndipo anauka Mose, ndi Yoswa mtumiki wake; ndipo Mose anakwera m'phiri la Mulungu.


Ndipo pamene Yoswa anamva phokoso la kufuula kwa anthu, anati kwa Mose, Kuli phokoso la nkhondo kuchigono.


Ndipo anthu onse anaona mtambo njo ulikuima pakhomo pa chihema; ndi anthu onse anaimirira, nalambira, yense pakhomo pa hema wake.


Ndipo kunali, pakulowa Mose m'chihemacho, mtambo njo udafutsika, nuima pakhomo pa chihemacho; ndipo Yehova analankhula ndi Mose.


Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.


Ndipo Yoswa mwana wa Nuni, mtumiki wa Mose kuyambira ubwana wake, anayankha nati, Mose, mfumu yanga, aletseni.


Satero mtumiki wanga Mose; ndiye wokhulupirika m'nyumba mwanga monse.


Ndimanena naye pakamwa ndi pakamwa, moonekera, osati mophiphiritsa; ndipo amapenyerera maonekedwe a Yehova; potero munalekeranji kuopa kutsutsana naye mtumiki wanga, Mose.


Izi anati, ndipo zitatha izi ananena nao, Lazaro bwenzi lathu ali m'tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.


Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mau a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira.


Ndipo Yehova anati kwa Mose, Taona, ayandikira masiku ako akuti uyenera kufa; kaitane Yoswa, nimuoneke m'chihema chokomanako, kuti ndimlangize. Namuka Mose ndi Yoswa, naoneka m'chihema chokomanako.


Ndipo sanaukenso mneneri mu Israele ngati Mose, amene Yehova anadziwana naye popenyana maso;


Yehova ananena ndi inu popenyana maso m'phirimo, ali pakati pa moto,


ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa