Eksodo 33:12 - Buku Lopatulika12 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Taonani, Inu munena ndi ine, Kwera nao anthu awa; koma simunandidziwitse amene mudzamtuma amuke nane. Koma munati, Ndikudziwa dzina lako, wapezanso ufulu pamaso panga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201412 Ndipo Mose anati kwa Yehova, Taonani, Inu munena ndi ine, Kwera nao anthu awa; koma simunandidziwitsa amene mudzamtuma amuke nane. Koma munati, Ndikudziwa dzina lako, wapezanso ufulu pamaso panga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa12 Mose adauza Chauta kuti, “Mwakhala mukundiwuza kuti ndiŵatsogolere anthuŵa ku dzikolo, koma simudandiwuze amene mudzamtuma kuti apite nane. Komabe mwanena kale kuti, ‘Ndikukudziŵa bwino iwe, ndipo ndakondwa nawe.’ Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero12 Mose anati kwa Yehova, “Inu mwakhala mukundiwuza kuti, ‘Tsogolera anthu awa,’ koma simunandiwuze amene mudzamutuma kuti apite pamodzi nane. Inu mwanena kuti, ‘Ndikukudziwa bwino kwambiri ndipo wapeza chisomo pamaso panga.’ Onani mutuwo |