Eksodo 4:20 - Buku Lopatulika20 Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, nawakweza pabulu, nabwerera kunka ku dziko la Ejipito; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake amuna, nawakweza pa bulu, nabwerera kunka ku dziko la Ejipito; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Motero Mose adatenga mkazi wake ndi ana ake, naŵakweza pa bulu onsewo, ndipo adapita ku Ejipito, atatenga ndodo imene adampatsa Mulungu ija. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Kotero Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, ndipo anawakweza pa bulu nayamba ulendo wobwerera ku Igupto. Ndipo anatenga ndodo ya Mulungu ija mʼdzanja lake. Onani mutuwo |