Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Eksodo 4:20 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Kotero Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, ndipo anawakweza pa bulu nayamba ulendo wobwerera ku Igupto. Ndipo anatenga ndodo ya Mulungu ija mʼdzanja lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

20 Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake aamuna, nawakweza pabulu, nabwerera kunka ku dziko la Ejipito; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Pamenepo Mose anatenga mkazi wake ndi ana ake amuna, nawakweza pa bulu, nabwerera kunka ku dziko la Ejipito; ndipo Mose anagwira ndodo ya Mulungu m'dzanja lake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Motero Mose adatenga mkazi wake ndi ana ake, naŵakweza pa bulu onsewo, ndipo adapita ku Ejipito, atatenga ndodo imene adampatsa Mulungu ija.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 4:20
10 Mawu Ofanana  

Nyamula ndodo yako ndi kutambasula dzanja lako kuloza ku nyanja, kugawa madzi kuti Aisraeli awoloke powuma.


Mose anati kwa Yoswa, “Sankha amuna amphamvu ndipo upite ukamenyane ndi Amaleki. Mawa ndidzayima pamwamba pa phiri nditagwira ndodo ya Mulungu.”


Yetero anali atatumiza uthenga kwa Mose kuti, “Ine Yetero, mpongozi wako, ndikubwera ndi mkazi wako ndi ana ake awiri.”


Zipora anabereka mwana wa mwamuna amene Mose anamutcha Geresomu, popeza anati, “Ndakhala mlendo mʼdziko la eni.”


Koma utenge ndodo imene ili mʼdzanja lakoyo kuti ukachite nayo zizindikiro zozizwitsa.”


Ndipo Yehova anamufunsa nati, “Nʼchiyani chili mʼdzanja lakolo?” Mose anayankha kuti, “Ndodo.”


Choncho Mose anatukula dzanja lake ndi kumenya thanthwelo kawiri ndi ndodo yake ndipo madzi ambiri anatuluka mwamphamvu, ndipo anthu ndi ziweto zawo anamwa.


Mose atamva mawu awa anathawira ku Midiyani, kumene anakhala mlendo ndipo anabereka ana amuna awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa