Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoswa 8:3 - Buku Lopatulika

3 Pamenepo anauka Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo, kuti akwere ku Ai; ndipo Yoswa anasankha amuna zikwi makumi atatu, ndiwo ngwazi, nawatumiza apite usiku,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pamenepo anauka Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo, kuti akwere ku Ai; ndipo Yoswa anasankha amuna zikwi makumi atatu, ndiwo ngwazi, nawatumiza apite usiku,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Motero Yoswa adakonzeka ndi ankhondo ake kupita ku Ai. Adasankhula ankhondo ena olimba mtima zikwi makumi atatu, ndipo adaŵatuma usiku.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Kotero Yoswa ndi gulu lonse la nkhondo anakonzeka kupita ku Ai. Iye anasankha amuna 30,000 odziwa kumenya nkhondo bwino ndipo anawatumiza usiku

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 8:3
10 Mawu Ofanana  

Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nutuluke kuyambana naye Amaleke; mawa ndidzaima pamwamba pa chitunda, ndi ndodo ya Mulungu m'dzanja langa.


ndipo iwo sanadziwe kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse, kotero kudzakhala kufika kwake kwa Mwana wa Munthu.


mbuye wa kapoloyo adzafika tsiku losamuyembekeza iye, ndi nthawi yosadziwa iye,


Koma pakati pa usiku panali kufuula, Onani, mkwati! Tulukani kukakomana naye.


Pakuti inu nokha mudziwa bwino kuti tsiku la Ambuye lidzadza monga mbala usiku.


Pamenepo Yoswa anakwera kuchokera ku Giligala, iye ndi anthu onse a nkhondo pamodzi naye, ndi ngwazi zonse.


ndipo uzimchitira Ai ndi mfumu yake monga umo unamchitira Yeriko ndi mfumu yake; koma zofunkha zake ndi ng'ombe zake mudzifunkhire nokha; udziikire anthu alalire kukhonde kwa mzinda.


nawalamulira ndi kuti, Taonani, muzikhala olalira kukhonde kwa mzinda; musakhalira kutali ndi mzinda, koma mukhale okonzekeratu nonse;


Koma tsiku la Ambuye lidzadza ngati mbala; m'mene miyamba idzapita ndi chibumo chachikulu, ndi zam'mwamba zidzakanganuka ndi kutentha kwakukulu, ndipo dziko ndi ntchito zili momwemo zidzatenthedwa.


Ndipo tsopano, taukani usiku, inu ndi anthu okhala nanu ndi kulalira kuthengo;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa