Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yoswa 8:2 - Buku Lopatulika

2 ndipo uzimchitira Ai ndi mfumu yake monga umo unamchitira Yeriko ndi mfumu yake; koma zofunkha zake ndi ng'ombe zake mudzifunkhire nokha; udziikire anthu alalire kukhonde kwa mzinda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 ndipo uzimchitira Ai ndi mfumu yake monga umo unamchitira Yeriko ndi mfumu yake; koma zofunkha zake ndi ng'ombe zake mudzifunkhire nokha; udziikire anthu alalire kukhonde kwa mudzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Mzinda wa Ai ndi mfumu yake yomwe, muuchite zomwe mudachita Yeriko ndi mfumu yake. Koma katundu wamumzindamo ndi zoŵeta, musunge zikhale zanu. Muulalire mzindawo, ndipo muuthire nkhondo cha kumbuyo kwake.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Mzinda wa Ai ndi mfumu yake muchite monga munachita ndi mzinda wa Yeriko ndi mfumu yake, koma katundu wa mumzindamo ndi zoweta mukazitenge ndi kuzisunga kuti zikhale zanu. Mukalalire mzinda wa Ai ndi kuwuthira nkhondo kuchokera kumbuyo.”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 8:2
27 Mawu Ofanana  

Koma Yerobowamu anazunguliritsa owalalira, awadzere kumbuyo; momwemo iwowa anali kumaso kwa Yuda, ndi owalalira anali kumbuyo kwao.


Ndipo poyamba iwo kuimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amowabu, ndi a m'phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha.


Indedi munthu ayenda ngati mthunzi; Indedi avutika chabe: Asonkhanitsa chuma, ndipo sadziwa adzachilandira ndani?


Wabwino asiyira zidzukulu zake cholowa chabwino; koma wochimwa angosungira wolungama chuma chake.


Munthu wokhulupirika ali ndi madalitso ambiri; koma wokangaza kulemera sadzapulumuka chilango.


Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikire, momwemo iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ake chidzamsiya iye, ndipo pa chitsirizo adzakhala wopusa.


Muwakwezere mbendera makoma a Babiloni, mulimbikitse ulonda, muike alonda, mupangiretu olalira, pakuti Yehova waganiziratu ndi kuchita chomwe ananena za okhala mu Babiloni.


Zoweta zokha tinadzifunkhira, pamodzi ndi zofunkha za mizinda tidailanda.


Koma akazi ndi ana ndi ng'ombe ndi zonse zili m'mzindamo, zankhondo zake zonse, mudzifunkhire nokha; ndipo mudye zankhondo za adani anu, zimene Yehova Mulungu wanu anakupatsani.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Usamuopa; popeza ndampereka iye ndi anthu ake onse, ndi dziko lake, m'dzanja lako; umchitire monga umo unachitira Sihoni mfumu ya Aamori, amene anakhala mu Hesiboni.


Ndipo kunali, pamene Adoni-Zedeki mfumu ya Yerusalemu anamva kuti Yoswa adalanda Ai, ndi kumuononga konse; nachitira Ai ndi mfumu yake monga adachitira Yeriko ndi mfumu yake; ndi kuti nzika za Gibiyoni zinachitirana mtendere ndi Israele, n'kukhala pakati pao;


Ndipo Yoswa anagwira Makeda tsiku lomwe lija ndi kuukantha ndi lupanga lakuthwa, ndi mfumu yake yomwe; anawaononga konse, ndi amoyo onse anali m'mwemo, osasiyapo ndi mmodzi yense, nachitira mfumu ya ku Makeda monga anachitira mfumu ya ku Yeriko.


Ndi zofunkha zonse za mizinda iyi ndi ng'ombe ana a Israele anadzifunkhira; koma anakantha ndi lupanga lakuthwa anthu onse mpaka adawaononga osasiyapo ndi mmodzi yense wopuma mpweya.


Ndipo anapereka kuziononga ndi lupanga lakuthwa zonse za m'mzinda, amuna ndi akazi omwe, ana ndi nkhalamba zomwe, kudza ng'ombe, ndi nkhosa, ndi abulu, ndi lupanga lakuthwa.


Ndipo anatenga amuna ngati zikwi zisanu, nawaika m'molalira pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa mzinda.


Ndipo kunali, pamene mfumu ya ku Ai anachiona, anafulumira iwo, nalawira mamawa, natuluka amuna a m'mzinda kuthirana ndi Israele, iye ndi anthu ake onse, poikidwiratu patsogolo pa chidikha; popeza sanadziwe kuti amlalira kukhonde kwa mzinda.


Nauka msanga olalirawo m'mbuto mwao, nathamanga pamene anatambasula dzanja lake, nalowa m'mzinda, naugwira; nafulumira nayatsa mzindawo.


Ndipo kunali, atatha Israele kupha nzika zonse za ku Ai, kuthengo, kuchipululu kumene anawapirikitsira, natha onse kugwa ndi lupanga lakuthwa mpaka adathedwa onse, Aisraele onse anabwerera ku Ai, naukantha ndi lupanga lakuthwa.


Pamenepo anauka Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo, kuti akwere ku Ai; ndipo Yoswa anasankha amuna zikwi makumi atatu, ndiwo ngwazi, nawatumiza apite usiku,


pamenepo muziuka m'molalira ndi kulowa m'mzinda; pakuti Yehova Mulungu wanu; adzaupereka m'manja mwanu.


Ndipo kudzali, mutagwira mzinda, muzitentha mzindawo ndi moto; muzichita monga mwa mau a Yehova; taonani, ndakulamulirani.


Ndipo Yoswa anawatuma, namuka iwo kulowa m'molalira, nakhala pakati pa Betele ndi Ai, kumadzulo kwa Ai; koma Yoswa anakhala mwa anthu usiku uja.


Koma pamene nzika za Gibiyoni zinamva zimene Yoswa adachitira Yeriko ndi Ai,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa