Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 8:4 - Buku Lopatulika

4 nawalamulira ndi kuti, Taonani, muzikhala olalira kukhonde kwa mzinda; musakhalira kutali ndi mzinda, koma mukhale okonzekeratu nonse;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 nawalamulira ndi kuti, Taonani, muzikhala olalira kukhonde kwa mudzi; musakhalira kutali ndi mudzi, koma mukhale okonzekeratu nonse;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Adaŵapatsa malamulo akuti, “Kabisaleni kumbuyo kwa mzindawo. Musakapite patali ndi mzindawo, koma kakhaleni okonzekera kuuthira nkhondo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 nawapatsa malamulo awa kuti, “Mvetsani bwino; mukabisale kuseri kwa mzindawo. Musakapite patali ndi mzindawo, koma nonsenu mukakhale okonzekera nkhondo.

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 8:4
14 Mawu Ofanana  

Niuka mfumu usiku, ninena ndi anyamata ake, Ndikufotokozereni m'mene Aaramu atichitira ife. Adziwa kuti tagwidwa ndi njala, natuluka m'misasa, nabisala kuthengo, ndi kuti, Pamene atuluka m'mzinda tidzawagwira ndi moyo ndi kulowa m'mzindamo.


Koma Yerobowamu anazunguliritsa owalalira, awadzere kumbuyo; momwemo iwowa anali kumaso kwa Yuda, ndi owalalira anali kumbuyo kwao.


Nzeru ilimbitsa wanzeru koposa akulu khumi akulamulira m'mzinda.


Pamenepo ndinati, Nzeru ipambana mphamvu; koma anyoza nzeru ya wosauka, osamvera mau ake.


Pamenepo musakopedwe nao; pakuti amlalira iye oposa makumi anai a iwo amene anadzitemberera okha kuti sadzadya kapena kumwa kufikira atamupha iye; ndipo akonzekeratu tsopano nayang'anira lonjezano lanu.


Pamenepo anthu onse okhala m'mzinda, anaitanidwa awapirikitse, nampirikitsa Yoswa, nakokedwa kusiyana ndi mzinda.


Pamenepo anauka Yoswa, ndi anthu onse a nkhondo, kuti akwere ku Ai; ndipo Yoswa anasankha amuna zikwi makumi atatu, ndiwo ngwazi, nawatumiza apite usiku,


Ndipo Israele anaika olalira Gibea pozungulira pake.


Nauka amuna onse a Israele m'malo ao nanika ku Baala-Tamara; natuluka Aisraele olalira aja m'malo mwao, kumwera kwa Geba.


Ndipo ana a Benjamini anaona kuti takanthidwa; popeza amuna a Israele anawapatsa Abenjamini malo, pakuti anatama olalira amene anawaikiratu pa Gibea.


Ndipo eni ake a ku Sekemu anaika omlalira pamwamba pa mapiri; amene anawawanya onse akudzera njirayi; ndipo anamuuza Abimeleki.


Ndipo tsopano, taukani usiku, inu ndi anthu okhala nanu ndi kulalira kuthengo;


Atero Yehova wa makamu, Ndinaonerera chimene Amaleke anachitira Israele, umo anamlalira panjira, m'mene iye anakwera kutuluka mu Ejipito.


Ndipo Saulo anafika kumzinda wa Amaleke, nalalira kuchigwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa