Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 17:8 - Buku Lopatulika

8 Pamenepo anadza Amaleke, nayambana ndi Israele mu Refidimu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Pamenepo anadza Amaleke, nayambana ndi Israele m'Refidimu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono kudabwera Aamaleke ku Refidimu kudzamenyana ndi Aisraele.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Amaleki anabwera ku Refidimu kudzamenyana ndi Aisraeli.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 17:8
13 Mawu Ofanana  

Ndipo anabwera nafika ku Enimisipati (kumeneko ndi ku Kadesi), nakantha dziko lonse la Aamaleke, ndiponso Aamori amene akhala mu Hazazoni-Tamara.


Ndipo Timna anali mkazi wake wamng'ono wa Elifazi mwana wamwamuna wa Esau; ndipo anambalira Elifazi Amaleke: amenewa ndi ana aamuna a Ada mkazi wake wa Esau.


mfumu Kora, mfumu Gatamu, mfumu Amaleke: amenewa ndi mafumu a kwa Elifazi m'dziko la Edomu: amenewa ndi ana aamuna a Ada.


Gebala ndi Amoni ndi Amaleke; Filistiya, pamodzi ndi iwo okhala mu Tiro.


Ndipo khamu lonse la ana a Israele linachoka m'chipululu cha Sini, M'zigono zao, monga mwa mau a Yehova, nagona mu Refidimu. Koma kumeneko kunalibe madzi akumwa anthu.


Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordani.


Ndipo anayang'ana ku Amaleke, nanena fanizo lake, nati, Amaleke ndiye woyamba wa amitundu; koma chitsiriziro chake, adzaonongeka ku nthawi zonse.


Ndipo kunali, akabzala Israele, amakwera Amidiyani, ndi Amaleke, ndi ana a kum'mawa, inde amawakwerera;


Ndipo iye anakula mphamvu, nakantha Aamaleke, napulumutsa Aisraele m'manja a akuwawawanya.


Atero Yehova wa makamu, Ndinaonerera chimene Amaleke anachitira Israele, umo anamlalira panjira, m'mene iye anakwera kutuluka mu Ejipito.


Ndipo Davide ndi anthu ake anakwera, nathira nkhondo yovumbulukira pa Agesuri, ndi Agerizi, ndi Aamaleke; pakuti awa ndiwo anthu akale m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Ejipito.


Ndipo kunali, pakufika Davide ndi anthu ake ku Zikilagi tsiku lachitatu, Aamaleke adaponya nkhondo yovumbulukira kumwera, ndi ku Zikilagi, nathyola Zikilagi nautentha ndi moto;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa