Ndipo mfumu inanena ndi Zadoki, Ubwerera nalo likasa la Mulungu kumzindako; akandikomera mtima Yehova, Iye adzandibwezanso, nadzandionetsanso ili, ndi pokhala pake pomwe.
Danieli 9:25 - Buku Lopatulika Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Tsono udziwe ndipo uzindikire izi kuti kuyambira pamene lamulo linaperekedwa kuti Yerusalemu akonzedwenso mpaka pamene mfumu Yodzozedwa idzafike padzapita zaka 49. Pa zaka 434 mzinda wa Yerusalemu udzamangidwanso, ndipo mabwalo ndi ngalande zake zidzatetezedwa. Koma nthawiyi idzakhala ya masautso. |
Ndipo mfumu inanena ndi Zadoki, Ubwerera nalo likasa la Mulungu kumzindako; akandikomera mtima Yehova, Iye adzandibwezanso, nadzandionetsanso ili, ndi pokhala pake pomwe.
Momwemo inalekeka ntchito ya nyumba ya Mulungu yokhala ku Yerusalemu; nilekeka mpaka chaka chachiwiri cha ufumu wa Dariusi mfumu ya Persiya.
Zitatha izi tsono, pokhala mfumu Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya, anadza Ezara mwana wa Seraya, mwana wa Azariya, mwana wa Hilikiya,
Ndipo iye anafika ku Yerusalemu mwezi wachisanu, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha mfumu.
Pamenepo Eliyasibu mkulu wa ansembe ananyamuka pamodzi ndi abale ake ansembe, namanga Chipata cha Nkhosa; anachipatula, naika zitseko zake, inde anachipatula mpaka Nsanja ya Zana, mpaka Nsanja ya Hananele.
Nanena iye pamaso pa abale ake ndi ankhondo a ku Samariya, nati, Alikuchitanji Ayuda ofookawa? Adzimangire linga kodi? Adzapereka nsembe kodi? Adzatsiriza tsiku limodzi kodi? Adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa?
napangana chiwembu iwo onse pamodzi, kudzathira nkhondo ku Yerusalemu, ndi kuchita chisokonezo m'menemo.
Ndipo linga linatsirizika pa tsiku la makumi awiri ndi lachisanu la mwezi wa Eluli, titalimanga masiku makumi asanu mphambu awiri.
Pakuti kwa ife mwana wakhanda wabadwa, kwa ife mwana wamwamuna wapatsidwa; ndipo ulamuliro udzakhala pa phewa lake, ndipo adzamutcha dzina lake Wodabwitsa, Wauphungu, Mulungu wamphamvu, Atate Wosatha, Kalonga wa mtendere.
Inde inadzikulitsa kufikira kwa kalonga wa khamulo, nimchotsera nsembe yopsereza yachikhalire, ndi pokhala malo ake opatulika panagwetsedwa.
Ndipo mwa kuchenjera kwake adzapindulitsa chinyengo m'dzanja mwake, nadzadzikuza m'mtima mwake; ndipo posatekeseka anthu, adzaononga ambiri; adzaukiranso kalonga wa akalonga, koma adzathyoledwa popanda dzanja.
Pakuyamba iwe mapembedzero ako, linatuluka lamulo; ndipo ndadza ine kukufotokozera; pakuti ukondedwa kwambiri; zindikira tsono mau awa, nulingirire masomphenyawo.
Uzisonkhana tsopano magulumagulu, mwana wamkazi wa magulu iwe; watimangira misasa, adzapanda woweruza wa Israele ndi ndodo patsaya.
Koma iwe, Betelehemu Efurata, ndiwe wamng'ono kuti ukhale mwa zikwi za Yuda, mwa iwe mudzanditulukira wina wakudzakhala woweruza mu Israele; matulukiro ake ndiwo a kale lomwe, kuyambira nthawi yosayamba.
Ndipo iye amene afesedwa pa nthaka yabwino, uyu ndiye wakumva mau nawadziwitsa; amene abaladi zipatso, nazifitsa, ena za makumi khumi, ena za makumi asanu ndi limodzi, ena za makumi atatu.
Chifukwa chake m'mene mukadzaona chonyansa cha kupululutsa, chimene chidanenedwa ndi Daniele mneneri, chitaima m'malo oyera (iye amene awerenga m'kalata azindikire)
Ndipo pamene mukaona chonyansa cha kupululutsa chilikuima pomwe sichiyenera (wakuwerenga azindikire), pamenepo a mu Yudeya athawire kumapiri:
Anayamba iye kupeza mbale wake yekha Simoni, nanena naye, Tapeza ife Mesiya (ndiko kusandulika Khristu).
Mkazi ananena ndi Iye, Ndidziwa kuti Mesiya adza (wotchedwa Khristu): akadzadza Iyeyu, adzatiuza zonse.
ndipo munamupha Mkulu wa moyo; amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa; za ichi ife tili mboni.
Ameneyo Mulungu anamkweza ndi dzanja lake lamanja, akhale Mtsogoleri ndi Mpulumutsi, kuti apatse kwa Israele kulapa, ndi chikhululukiro cha machimo.
Ndipo Filipo anamthamangira, namva iye alikuwerenga Yesaya mneneri, ndipo anati, Kodi muzindikira chimene muwerenga?
ndi kwa Yesu Khristu, mboni yokhulupirikayo, wobadwa woyamba wa akufa, ndi mkulu wa mafumu a dziko lapansi. Kwa Iye amene atikonda ife, natimasula kumachimo athu ndi mwazi wake;
Ndipo ali nalo pa chovala chake ndi pa ntchafu yake dzina lolembedwa, MFUMU YA MAFUMU, NDI MBUYE WA AMBUYE.