Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ezara 7:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo iye anafika ku Yerusalemu mwezi wachisanu, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo iye anafika ku Yerusalemu mwezi wachisanu, ndicho chaka chachisanu ndi chiwiri cha mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Ezarayo adafika ku Yerusalemu pa mwezi wachisanu wa chaka chachisanu ndi chiŵiri cha mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Ezara anafika ku Yerusalemu pa mwezi wachisanu wa chaka chachisanu ndi chiwiri cha mfumu.

Onani mutuwo Koperani




Ezara 7:8
7 Mawu Ofanana  

Ndipo anasonkhana ku Yerusalemu amuna onse a Yuda ndi Benjamini asanapite masiku atatu, ndiwo mwezi wachisanu ndi chinai, tsiku la makumi awiri a mwezi; nakhala pansi anthu onse m'khwalala pakhomo pa nyumba ya Mulungu, alikunjenjemera chifukwa cha mlandu uwu, ndi chifukwa cha mvulayi.


Nakweranso kunka ku Yerusalemu ena a ana a Israele, ndi ansembe, ndi Alevi, ndi oimbira, ndi odikira, ndi antchito a m'kachisi, chaka chachisanu ndi chiwiri cha Arita-kisereksesi mfumu.


Pakuti tsiku loyamba la mwezi woyamba, ndilo chiyambi cha ulendo wokwera kuchokera ku Babiloni, ndi tsiku loyamba la mwezi wachisanu anafika ku Yerusalemu, monga linamkhalira dzanja lokoma la Mulungu wake.


Ndipo tinafika ku Yerusalemu ndi kukhalako masiku atatu.


Popeza ife ndife akapolo, koma Mulungu wathu sanatisiye mu ukapolo wathu, natifikitsira chifundo pamaso pa mafumu a Persiya, kuti atitsitsimutse kuimika nyumba ya Mulungu wathu, ndi kukonzanso muunda wake, ndi kutipatsa linga mu Yuda ndi mu Yerusalemu.


Momwemo anatengedwa Estere kunka kwa mfumu Ahasuwero, kunyumba yake yachifumu, mwezi wakhumi, ndiwo mwezi wa Tebeti, chaka chachisanu ndi chiwiri cha ufumu wake.


Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa