Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 13:14 - Buku Lopatulika

14 Ndipo pamene mukaona chonyansa cha kupululutsa chilikuima pomwe sichiyenera (wakuwerenga azindikire), pamenepo a mu Yudeya athawire kumapiri:

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

14 Ndipo pamene mukaona chonyansa cha kupululutsa chilikuima pomwe sichiyenera (wakuwerenga azindikire), pamenepo a m'Yudeya athawire kumapiri:

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

14 “Chosakaza chonyansa chija chidzakhala atachiimika pamalo pomwe sichiyenera kukhalapo. (Umvetse bwino amene ukuŵerengawe.) Mukadzaona zimenezi, pamenepo amene ali m'Yudeya adzathaŵire ku mapiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

14 “Mukadzaona ‘chinthu chonyansa chosakaza’ chitayima pa malo amene si ake, owerenga azindikire. Pamenepo amene ali ku Yudeya athawire kumapiri.

Onani mutuwo Koperani




Marko 13:14
14 Mawu Ofanana  

Amaliwongo atambasulira manja ao pa zokondweretsa zake zonse; pakuti waona amitundu atalowa m'malo ake opatulika, amene munalamulira kuti asalowe mumsonkhano mwanu.


Atero Ambuye Yehova, Palibe mlendo wosadulidwa m'mtima, wosadulidwa m'thupi, alowe m'malo anga opatulika, mwa alendo onse ali pakati pa ana a Israele.


Ndipo ankhondo adzamuimirira, nadzadetsa malo opatulika ndi linga lake; nadzachotsa nsembe yosalekezayo, nadzaimitsa chonyansa chopululutsacho.


Ndipo kuyambira nthawi yoti idzachotsedwa nsembe yachikhalire, ndipo chidzaimika chonyansa chakupululutsa, adzakhalanso masiku chikwi chimodzi mphambu mazana awiri kudza makumi asanu ndi anai.


Pamenepo ndinamva wina woyera alikunena; ndi wina woyera anati kwa iye uja wanenayo, Masomphenya a nsembe yopsereza yachikhalire, ndi cholakwa chakupululutsa cha kupereka malo opatulika ndi khamulo ziponderezedwe, adzakhala mpaka liti?


Ndipo iye adzapangana chipangano cholimba ndi ambiri sabata limodzi; ndi pakati pa sabata adzaleketsa nsembe yophera ndi nsembe yaufa; ndi pa phiko la zonyansa padzafika wina wakupasula, kufikira chimaliziro cholembedweratu, mkwiyo udzatsanulidwa pa wopasulayo.


Mwamvetsa zonsezi kodi? Iwo anati kwa Iye, Inde.


Abale, musakhale ana m'chidziwitso, koma m'choipa khalani makanda, koma m'chidziwitso akulu misinkhu.


Wodala iye amene awerenga, ndi iwo amene akumva mau a chinenerocho, nasunga zolembedwa momwemo; pakuti nthawi yayandikira.


Pano pali nzeru. Iye wakukhala nacho chidziwitso awerenge chiwerengero cha chilombocho; pakuti chiwerengero chake ndi cha munthu; ndipo chiwerengero chake ndicho mazana asanu ndi limodzi mphambu makumi asanu ndi limodzi kudza zisanu ndi chimodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa