Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Nehemiya 6:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo linga linatsirizika pa tsiku la makumi awiri ndi lachisanu la mwezi wa Eluli, titalimanga masiku makumi asanu mphambu awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo linga linatsirizika pa tsiku la makumi awiri ndi lachisanu la mwezi wa Eluli, titalimanga masiku makumi asanu mphambu awiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Patapita masiku 52, pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli, khoma lija adatsiriza kumanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Ndipo khoma linatsirizidwa kumanga pa tsiku la 25 la mwezi wa Eluli. Linamangidwa pa masiku okwana 52.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 6:15
7 Mawu Ofanana  

Ndipo akulu a Ayuda anamanga opanda chosoweka, mwa kunenera kwa mneneri Hagai, ndi Zekariya mwana wa Ido. Naimanga, naitsiriza, monga mwa lamulo la Mulungu wa Israele, ndi monga mwa lamulo la Kirusi, ndi Dariusi, ndi Arita-kisereksesi mfumu ya Persiya.


Nitsirizidwa nyumba iyi tsiku lachitatu la mwezi wa Adara, ndicho chaka chachisanu ndi chimodzi cha ufumu wa Dariusi mfumu.


Ndipo atatha kumanga linga, ndinaika zitseko, nakhazika odikira, ndi oimbira, ndi Alevi;


Ndiye akunga mtengo wooka pa mitsinje ya madzi; wakupatsa chipatso chake pa nyengo yake, tsamba lake lomwe losafota; ndipo zonse azichita apindula nazo.


Yehova amanga Yerusalemu; asokolotsa otayika a Israele.


Dziwa tsono, nuzindikire, kuti kuyambira kutuluka lamulo lakukonzanso, ndi kummanga Yerusalemu, kufikira wodzozedwayo, ndiye kalonga, kudzakhala masabata asanu ndi awiri; ndi masabata makumi asanu ndi limodzi mphambu awiri makwalala ndi tchemba zidzamangidwanso, koma mu nthawi za mavuto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa