Nehemiya 4:2 - Buku Lopatulika2 Nanena iye pamaso pa abale ake ndi ankhondo a ku Samariya, nati, Alikuchitanji Ayuda ofookawa? Adzimangire linga kodi? Adzapereka nsembe kodi? Adzatsiriza tsiku limodzi kodi? Adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Nanena iye pamaso pa abale ake ndi ankhondo a ku Samariya, nati, Alikuchitanji Ayuda ofookawa? Adzimangire linga kodi? Adzapereka nsembe kodi? Adzatsiriza tsiku limodzi kodi? Adzakometsanso miyala ya ku miunda yotenthedwa? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Adalankhula pamaso pa abale ake, ndi pamaso pa gulu lankhondo la ku Samariya, adati, “Kodi Ayuda achabechabeŵa akuchita chiyani? Monga amati nkumanganso mzindawu? Kodi nsembe ndiye adzapereka? Kodi adzaumaliza pa tsiku limodzi? Kodi adzachita kutolatolanso miyala yakale ija, ndi m'mene idapsera muja?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Ndipo anayankhula pamaso pa abale ake ndi asilikali a Samariya kuti, “Kodi Ayuda ofowokawa akuchita chiyani? Kodi iwo nʼkumanganso khoma? Kodi adzaperekanso nsembe? Kodi adzatsiriza ntchitoyi tsiku limodzi? Kodi adzachita kutenga miyala yakale ija ndi mmene inapseramo?” Onani mutuwo |