chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.
Akolose 2:4 - Buku Lopatulika Ichi ndinena, kuti munthu asakusokeretseni inu ndi mau okopakopa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ichi ndinena, kuti munthu asakusokeretseni inu ndi mau okopakopa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikunenatu zimenezi, kuwopa kuti wina aliyense angakukopeni ndi mau onyenga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndikukuwuzani zimenezi kuti wina aliyense asakunamizeni ndi kukukopani ndi mawu ake. |
chifukwa Akhristu onama adzauka, ndi aneneri onama nadzaonetsa zizindikiro zazikulu ndi zozizwa: kotero kuti akanyenge, ngati nkotheka, osankhidwa omwe. Onani ndakuuziranitu pasadafike.
pakuti adzauka Akhristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzachita zizindikiro ndi zozizwitsa, kuti akasocheretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe.
ndipo mwa inu nokha adzauka anthu, olankhula zokhotakhota, kupatutsa ophunzira awatsate.
Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhale ndi mau okopa a nzeru, koma m'chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu;
Koma ndiopa, kuti pena, monga njoka inanyenga Heva ndi kuchenjerera kwake, maganizo anu angaipsidwe kusiyana nako kuona mtima ndi kuyera mtima zili kwa Khristu.
ndicho chifukwa cha abale onyenga olowezedwa m'tseri, amene analowa m'tseri kudzazonda ufulu wathu umene tili nao mwa Khristu Yesu, kuti akatichititse ukapolo.
Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;
Pamenepo ndinena ichi, ndipo ndichita umboni mwa Ambuye, kuti simuyendanso inu monganso amitundu angoyenda, m'chitsiru cha mtima wao,
Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.
Munthu aliyense asakunyengeni ndi kulanda mphotho yanu ndi kudzichepetsa mwini wake, ndi kugwadira kwa angelo, ndi kukhalira mu izi adaziona, wodzitukumula chabe ndi zolingalira za thupi lake, wosagwiritsa mutuwo,
Penyani kuti pasakhale wina wakulanda inu ngati chuma, mwa kukonda nzeru kwake, ndi chinyengo chopanda pake, potsata mwambo wa anthu, potsata zoyamba za dziko lapansi, osati potsata Khristu;
Ana inu, ndi nthawi yotsiriza iyi; ndipo monga mudamva kuti wokana Khristu akudza, ngakhale tsopano alipo okana Khristu ambiri; mwa ichi tizindikira kuti ndi nthawi yotsirizira iyi.
Okondedwa, musamakhulupirira mzimu uliwonse, koma yesani mizimu ngati ichokera mwa Mulungu: popeza aneneri onyenga ambiri anatuluka kulowa m'dziko lapansi.
Pakuti onyenga ambiri adatuluka kulowa m'dziko lapansi, ndiwo amene savomereza kuti Yesu Khristu anadza m'thupi. Ameneyo ndiye wonyenga ndi wokana Khristu.
Ndipo chinaponyedwa pansi chinjoka chachikulu, njoka yokalambayo, iye wotchedwa mdierekezi ndi Satana, wonyenga wa dziko lonse; chinaponyedwa pansi kudziko, ndi angelo ake anaponyedwa naye pamodzi.
Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi.
namponya ku chiphompho chakuya, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu kufikira kudzatha zaka chikwi; patsogolo pake ayenera kumasulidwa iye kanthawi.
nadzatuluka kudzasokeretsa amitundu ali mungodya zinai za dziko, Gogi, ndi Magogi, kudzawasonkhanitsa achite nkhondo: chiwerengero chao cha iwo amene chikhala ngati mchenga wa kunyanja.