Marko 13:22 - Buku Lopatulika22 pakuti adzauka Akhristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzachita zizindikiro ndi zozizwitsa, kuti akasocheretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201422 pakuti adzauka Akhristu onyenga ndi aneneri onyenga, ndipo adzachita zizindikiro ndi zozizwitsa, kuti akasocheretse, ngati nkutheka, osankhidwa omwe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa22 Chifukwa kudzaoneka anthu onama omanena kuti, ‘Ndine Khristu uja,’ kapena kuti, ‘Ndine mneneri.’ Anthuwo azidzachita ntchito zamphamvu ndiponso zinthu zozizwitsa, kuti ngati nkotheka asokeze ngakhale osankhidwa a Mulungu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero22 Pakuti akhristu onama ndi aneneri onama adzaonekera ndipo adzachita zizindikiro ndi zodabwitsa kuti anyenge osankhidwiratu ngati kutakhala kotheka kutero. Onani mutuwo |
Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.