Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Akorinto 2:4 - Buku Lopatulika

4 Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhale ndi mau okopa a nzeru, koma m'chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndipo mau anga ndi kulalikira kwanga sanakhala ndi mau okopa a nzeru, koma m'chionetso cha Mzimu ndi cha mphamvu;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndipo pamene ndinkalankhula kapena kulalika, sindinkalankhula moonetsa nzeru, kuyesa kukopa anthu, koma mau anga anali otsimikizika ndi mphamvu za Mzimu Woyera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Uthenga ndi ulaliki wanga sunali wa mawu anzeru ndi onyengerera koma woonetsa mphamvu za Mzimu,

Onani mutuwo Koperani




1 Akorinto 2:4
28 Mawu Ofanana  

Kazitape woyendayenda awanditsa zinsinsi; usadudukire woyasama milomo yake.


Amkakamiza ndi kukoka kwa mau ake, ampatutsa ndi kusyasyalika kwa milomo yake.


Pakuti ndamva kugogodera kwa ambiri, mantha pozungulira ponse. Neneza, ndipo tidzamneneza iye, ati atsamwali anga onse, amene ayang'anira kutsimphina kwanga; kapena adzakopedwa, ndipo ife tidzampambana iye, ndipo tidzambwezera chilango.


Iwo aona zopanda pake, ndi phenda labodza amene anena, Atero Yehova; koma Yehova sanawatume, nayembekezetsa anthu kuti mauwo adzakhazikika.


Pakuti sindinakubisirani pakukulalikirani uphungu wonse wa Mulungu.


Ndipo Agripa anati kwa Paulo, Ndi kundikopa pang'ono ufuna kundiyesera Mkhristu.


Ndipo Mulungu wa chiyembekezo adzaze inu ndi chimwemwe chonse ndi mtendere m'kukhulupirira, kuti mukachuluke ndi chiyembekezo, mu mphamvu ya Mzimu Woyera.


mu mphamvu ya zizindikiro ndi zozizwitsa, mu mphamvu ya Mzimu Woyera; kotero kuti ine kuyambira ku Yerusalemu ndi kuzungulirako kufikira ku Iliriko, ndinakwanitsa Uthenga Wabwino wa Khristu;


Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.


Pakuti Khristu sananditume ine kubatiza, koma kulalikira Uthenga Wabwino, si mu nzeru ya mau, kuti mtanda wa Khristu ungayesedwe wopanda pake.


Ndipo ine, abale, m'mene ndinadza kwa inu, sindinadze ndi kuposa kwa mau, kapena kwa nzeru, polalikira kwa inu chinsinsi cha Mulungu.


Zimenenso tilankhula, si ndi mau ophunzitsidwa ndi nzeru za munthu, koma ophunzitsidwa ndi Mzimu; ndi kulinganiza zamzimu ndi zamzimu.


Pakuti ufumu wa Mulungu suli m'mau, koma mumphamvu. Mufuna chiyani?


m'mayeredwe, m'chidziwitso, m'chilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'chikondi chosanyenga;


Pakuti kodi ndikopa anthu tsopano, kapena Mulungu? Kapena kodi ndifuna kukondweretsa anthu? Ndikadakhala wokondweretsabe anthu, sindikadakhala kapolo wa Khristu.


Ichi ndinena, kuti munthu asakusokeretseni inu ndi mau okopakopa.


kuti Uthenga Wabwino wathu sunadze kwa inu m'mau mokha, komatunso mumphamvu, ndi mwa Mzimu Woyera, ndi m'kuchuluka kwakukulu; monga mudziwa tinakhala onga otani mwa inu chifukwa cha inu.


Kwa iwo amene kudavumbulutsidwa, kuti sanadzitumikire iwo okha, koma inu, ndi zinthu izi, zimene zauzidwa kwa inu tsopano, mwa iwo amene anakulalikirani Uthenga Wabwino mwa Mzimu Woyera, wotumidwa kuchokera Kumwamba; zinthu izi angelo alakalaka kusuzumiramo.


Pakuti sitinatsate miyambi yachabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Khristu, koma tinapenya m'maso ukulu wake.


Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;


Koma kunali, tsiku lachisanu ndi chiwiri anati kwa mkazi wa Samisoni, Kopa mwamuna wako, atitanthauzire mwambiwo; tingatenthe iwe ndi nyumba ya atate wako ndi moto. Kodi mwatiitana kulanda zathu; si momwemo?


Ndipo akalonga a Afilisti anamkwerera mkaziyo, nanena naye, Umkope nuone umo muchokera mphamvu yake yaikulu, ndi umo tingakhoze kumtha khama, kuti timmange kumzunza; ndipo tidzakupatsa aliyense ndalama mazana khumi ndi limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa