Chivumbulutso 13:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo adzachilambira onse akukhala padziko, amene dzina lao silinalembedwa m'buku la moyo la Mwanawankhosa, wophedwa kuyambira makhazikidwe a dziko lapansi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Onse okhala pa dziko lapansi adzachipembedza, ndiye kuti aliyense amene, chilengedwere dziko lapansi, dzina lake silidalembedwe m'buku la amoyo la Mwanawankhosa adaphedwa uja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Anthu onse okhala pa dziko lapansi adzapembedza chirombocho, aliyense amene chilengedwere cha dziko lapansi dzina lake silinalembedwe mʼbuku la amoyo la Mwana Wankhosa anaphedwa uja. Onani mutuwo |
Chilombo chimene unachiona chinaliko, koma kulibe; ndipo chidzatuluka m'chiphompho chakuya, ndi kunka kuchitayiko. Ndipo adzazizwa iwo akukhala padziko amene dzina lao silinalembedwe m'buku la moyo chiyambire makhazikidwe a dziko lapansi, pakuona chilombo, kuti chinaliko, ndipo kulibe, ndipo chidzakhalako.