Ndipo poyamba iwo kuimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amowabu, ndi a m'phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha.
2 Samueli 22:4 - Buku Lopatulika Ndidzaitana kwa Yehova amene ayenera timtamande; chomwecho ndidzapulumutsidwa kwa adani anga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndidzaitana kwa Yehova amene ayenera timtamande; chomwecho ndidzapulumutsidwa kwa adani anga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndimaitana Chauta, amene ayenera kumtamanda, ndipo amandipulumutsa kwa adani anga. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero “Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando, ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga. |
Ndipo poyamba iwo kuimba, ndi kulemekeza Yehova, anaika olalira alalire Aamoni, Amowabu, ndi a m'phiri la Seiri, akudzera Ayuda; ndipo anawakantha.
Nati Alevi, Yesuwa, ndi Kadimiyele, Bani, Hasabineya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya, ndi Petahiya, Imirirani, lemekezani Yehova Mulungu wanu kunthawi za nthawi; ndipo lilemekezeke dzina lanu la ulemerero, lokuzika loposa chilemekezo ndi chiyamiko chonse.
Adzafotokoza ndani ntchito zamphamvu za Yehova, adzamveketsa ndani chilemekezo chake chonse?
Pamenepo ndinaitana dzina la Yehova; ndikuti, Yehova ndikupemphani landitsani moyo wanga.
Munthu uyu wozunzika anafuula, ndipo Yehova anamumva, nampulumutsa m'masautso ake onse.
Yehova ndiye wamkulu, ayenera kulemekezekadi, m'mzinda wa Mulungu wathu, m'phiri lake loyera.
Pamenepo adani anga adzabwerera m'mbuyo tsiku lakuitana ine. Ichi ndidziwa, kuti Mulungu avomerezana nane.
Pakuti Yehova ndi wamkulu, nayenera kulemekezedwa kwakukulu; ayenera amuope koposa milungu yonse.
Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, ndipo zinalengedwa.
akunena ndi mau aakulu, Ayenera Mwanawankhosa, wophedwayo, kulandira chilimbiko, ndi chuma, ndi nzeru, ndi mphamvu, ndi ulemu, ndi ulemerero, ndi chiyamiko.