Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 22:4 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 “Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando, ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

4 Ndidzaitana kwa Yehova amene ayenera timtamande; chomwecho ndidzapulumutsidwa kwa adani anga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Ndidzaitana kwa Yehova amene ayenera timtamande; chomwecho ndidzapulumutsidwa kwa adani anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Ndimaitana Chauta, amene ayenera kumtamanda, ndipo amandipulumutsa kwa adani anga.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 22:4
20 Mawu Ofanana  

Atangoyamba kuyimba ndi kutamanda, Yehova anapereka mʼmanja mwawo anthu a ku Amoni ndi a ku Mowabu ndiponso a ku Phiri la Seiri amene amalimbana ndi Yuda, ndipo anagonjetsedwa.


Ndipo Alevi awa: Yesuwa, Kadimieli, Bani, Hasabaneya, Serebiya, Hodiya, Sebaniya ndi Petahiya anati: “Imirirani ndipo mutamande Yehova Mulungu wanu, amene ndi wamuyaya.” “Litamandike dzina lake laulemerero limene liposa madalitso ndi matamando onse.


Ndani angathe kufotokoza za ntchito zamphamvu za Yehova kapena kumutamanda mokwanira?


Ndidzakweza chikho cha chipulumutso ndipo ndidzayitana dzina la Yehova.


Ndidzapereka nsembe yachiyamiko kwa Inu ndipo ndidzayitanira pa dzina la Yehova.


Pakuti ananditchera khutu, ndidzayitana Iye masiku onse a moyo wanga.


Pamenepo ndinayitana dzina la Yehova: “Inu Yehova, pulumutseni!”


Ndimayitana Yehova amene ndi woyenera matamando, ndipo ndapulumutsidwa kwa adani anga.


Munthu wosauka uno anayitana, ndipo Yehova anamumva; Yehova anamupulumutsa ku mavuto ake onse.


Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.


Ndipo undiyitane pa tsiku lako la masautso; Ine ndidzakulanditsa, ndipo udzandilemekeza.”


Koma ine ndinafuwulira kwa Mulungu, ndipo Yehova anandipulumutsa.


Adani anga adzabwerera mʼmbuyo pamene ndidzalirira kwa Inu. Pamenepo ndidzadziwa kuti Mulungu ali ku mbali yanga.


Imbani ulemerero wa dzina lake; kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero.


Pakuti wamkulu ndi Yehova ndipo ndi woyenera kwambiri kumutamanda; ayenera kuopedwa kupambana milungu yonse.


pakuti, “Aliyense amene adzayitana pa dzina la Ambuye adzapulumuka.”


“Ndinu woyeneradi kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu, Ambuye ndi Mulungu wathu, pakuti munalenga zinthu zonse, ndipo mwakufuna kwanu zinalengedwa monga zilili.”


Ndipo angelowo anayimba ndi mawu ofuwula akuti, “Mwana Wankhosa amene anaphedwayu ndi woyenera kulandira ulamuliro, chuma, nzeru, mphamvu, ulemu, ulemerero ndi mayamiko.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa