Ndipo Abisalomu mlongo wake ananena naye, Kodi mlongo wako Aminoni anali ndi iwe? Koma tsopano ukhale chete, mlongo wanga, iye ali mlongo wako; usavutika ndi chinthuchi. Chomwecho Tamara anakhala wounguluma m'nyumba ya Abisalomu mlongo wake.
2 Samueli 19:19 - Buku Lopatulika Nati kwa mfumu, Mbuye wanga asandiwerengere ine mphulupulu ndiponso musakumbukire chimene mnyamata wanu ndinachita mwamphulupulu tsiku lija mbuye wanga mfumu anatuluka ku Yerusalemu, ngakhale kuchisunga mumtima mfumu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nati kwa mfumu, Mbuye wanga asandiwerengere ine mphulupulu ndiponso musakumbukire chimene mnyamata wanu ndinachita mwamphulupulu tsiku lija mbuye wanga mfumu anatuluka ku Yerusalemu, ngakhale kuchisunga mumtima mfumu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adauza mfumu kuti, “Mbuyanga, chonde mundikhululukire, musakumbukirenso tchimo limene ine kapolo wanu ndidachita pa tsiku lija, pamene inu mbuyanga mfumu munkachoka mu Yerusalemu. Amfumu musazisunge kukhosi zimenezi. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero ndipo anati, “Mbuye wanga musaganizire za kulakwa kwanga. Musakumbukire zolakwa zimene mtumiki wanu anakuchitirani tsiku limene mbuye wanga mfumu mumachoka mu Yerusalemu. Mfumu musazikumbukirenso zimenezi. |
Ndipo Abisalomu mlongo wake ananena naye, Kodi mlongo wako Aminoni anali ndi iwe? Koma tsopano ukhale chete, mlongo wanga, iye ali mlongo wako; usavutika ndi chinthuchi. Chomwecho Tamara anakhala wounguluma m'nyumba ya Abisalomu mlongo wake.
Chifukwa chake tsono mfumu mbuye wanga asasauke mtima ndi chinthuchi, ndi kuganiza kuti ana aamuna onse a mfumu afa; pakuti Aminoni yekha wafa.
Ndipo ngalawa yakuolotsera inaoloka kuti akatenge banja la mfumu ndi kuchita chomkomera. Ndipo Simei mwana wa Gera anagwa pansi pamaso pa mfumu pakuoloka iye pa Yordani.
Wodala munthuyu Yehova samwerengera mphulupulu zake; ndimo mumzimu mwake mulibe chinyengo.
Musakumbukire motitsutsa mphulupulu za makolo athu; nsoni zokoma zanu zitipeze msanga, pakuti tafooka kwambiri.
Ngati mkulu akukwiyira, usasiye malo ako; chifukwa chifatso chipembedza utachimwa kwambiri.
Ine, Inedi, ndine amene ndifafaniza zolakwa zako, chifukwa cha Ine mwini; ndipo Ine sindidzakumbukira machimo ako.
ndipo sadzaphunzitsa yense mnansi wake, ndi yense mbale wake, kuti, Mudziwe Yehova; pakuti iwo onse adzandidziwa, kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu wa iwo, ati Yehova; pakuti ndidzakhululukira mphulupulu yao, ndipo sindidzakumbukira tchimo lao.
Ndipo Aroni anati kwa Mose, Mfumu yanga, musatiikiretu kuchimwa kumene tapusa nako, ndi kuchimwa nako.
nanena, Ndinachita koipa ine, pakupereka mwazi wosalakwa. Koma iwo anati, Tili nacho chiyani ife? Udzionere wekha.
ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Khristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye yekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a chiyanjanitso.
Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu? Musatero iai; mfumu asanenera mnyamata wake kanthu, kapena nyumba yonse ya atate wanga; popeza ine mnyamata wanu sindidziwa kanthu ka izi zonse, ndi pang'ono ponse.
Mbuye wanga, musasamalire munthu uyu woipa, ndiye Nabala; chifukwa monga dzina lake momwemo iye; dzina lake ndiye Nabala, ndipo ali nako kupusa; koma ine mdzakazi wanu sindinaone anyamata a mbuye wanga, amene munawatumiza.
Pamenepo Saulo anati, Ndinachimwa; bwera, mwana wanga Davide; pakuti sindidzakuchitiranso choipa, popeza moyo wanga unali wa mtengo wapatali pamaso pako lero; ona, ndinapusa ndi kulakwa kwakukulu.