1 Samueli 25:25 - Buku Lopatulika25 Mbuye wanga, musasamalire munthu uyu woipa, ndiye Nabala; chifukwa monga dzina lake momwemo iye; dzina lake ndiye Nabala, ndipo ali nako kupusa; koma ine mdzakazi wanu sindinaone anyamata a mbuye wanga, amene munawatumiza. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201425 Mbuye wanga, musasamalire munthu uyu woipa, ndiye Nabala; chifukwa monga dzina lake momwemo iye; dzina lake ndiye Nabala, ndipo ali nako kupusa; koma ine mdzakazi wanu sindinaona anyamata a mbuye wanga, amene munawatumiza. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa25 Mbuyanga asasamale za amuna anga, munthu wa mkhalidwe wovuta uja. Monga momwe dzina lake liliri, iyenso ali choncho. Monga dzina lake limatanthauzira kuti chitsiru, zake zonse nzauchitsiru basi. Koma ine mdzakazi wanu, sindidaŵaone anyamata anu amene mudaaŵatumawo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero25 Mbuye wanga musasamale za mwamuna wanga Nabala, munthu wa khalidwe loyipa. Iyeyu ali monga dzina lake liliri. Monga dzina lake litanthauza kuti chitsiru, ndiye kuti zake zonse ndi zauchitsiru basi. Koma ine mdzakazi wanu, sindinawaone anthu amene mbuye wanga munawatuma. Onani mutuwo |