Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 22:15 - Buku Lopatulika

15 Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu? Musatero iai; mfumu asanenera mnyamata wake kanthu, kapena nyumba yonse ya atate wanga; popeza ine mnyamata wanu sindidziwa kanthu ka izi zonse, ndi pang'ono ponse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu? Musatero iai; mfumu asanenera mnyamata wake kanthu, kapena nyumba yonse ya atate wanga; popeza ine mnyamata wanu sindidziwa kanthu ka izi zonse, ndi pang'ono ponse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Kodi ndayamba lero kumfunsira kwa Mulungu zoti achite? Iyai, amfumu! Musandinenere kanthu kena kalikonse koipa, ine mtumiki wanu, kapenanso wina aliyense wa m'banja la bambo wanga, pakuti sindikudziŵa kanthu pa nkhaniyi mpang'ono pomwe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Kodi tsiku limeneli linali loyamba kuti ndimufunsire kwa Yehova? Ayi sichoncho! Mfumu musandinenere kanthu kalikonse koyipa kapena banja la abambo anga, pakuti sindikudziwa kanthu kena kalikonse ka zimenezi.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 22:15
10 Mawu Ofanana  

Ndipo pamodzi ndi Abisalomu panapita anthu mazana awiri a ku Yerusalemu ndiwo oitanidwa, namuka m'kupulukira kwao, osadziwa kanthu.


Ndipo ngalawa yakuolotsera inaoloka kuti akatenge banja la mfumu ndi kuchita chomkomera. Ndipo Simei mwana wa Gera anagwa pansi pamaso pa mfumu pakuoloka iye pa Yordani.


Nati kwa mfumu, Mbuye wanga asandiwerengere ine mphulupulu ndiponso musakumbukire chimene mnyamata wanu ndinachita mwamphulupulu tsiku lija mbuye wanga mfumu anatuluka ku Yerusalemu, ngakhale kuchisunga mumtima mfumu.


Ndipo Davide anafunsira kwa Yehova nati, Kodi ndimuke kuyambana nao Afilistiwo? Mudzawapereka m'dzanja langa kodi? Ndipo Yehova ananena ndi Davide, Pita, pakuti zoonadi ndidzapereka Afilisti m'dzanja lako.


Ndipo pamene Davide anafunsira kwa Yehova, Iye anati, Usamuke, koma ukawazungulire kumbuyo kuti ukawatulukire pandunji pa mkandankhuku.


Pakuti kudzitamandira kwathu ndiko umboni wa chikumbumtima chathu, kuti m'chiyero ndi kuona mtima kwa Mulungu, si m'nzeru ya thupi, koma m'chisomo cha Mulungu tinadzisunga m'dziko lapansi, koma koposa kwa inu.


Ndipo mfumu inati, Ukufa ndithu Ahimeleki, iwe ndi banja lonse la atate wako.


Ndipo Abigaile anafika kwa Nabala; ndipo, onani, anali ndi madyerero m'nyumba mwake, monga madyerero a mfumu; ndi mtima wa Nabala unasekera kwambiri m'kati mwake, pakuti analedzera kwambiri; m'mwemo uyo sadamuuze kanthu konse, kufikira kutacha.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa