2 Samueli 13:20 - Buku Lopatulika20 Ndipo Abisalomu mlongo wake ananena naye, Kodi mlongo wako Aminoni anali ndi iwe? Koma tsopano ukhale chete, mlongo wanga, iye ali mlongo wako; usavutika ndi chinthuchi. Chomwecho Tamara anakhala wounguluma m'nyumba ya Abisalomu mlongo wake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Ndipo Abisalomu mlongo wake ananena naye, Kodi mlongo wako Aminoni anali ndi iwe? Koma tsopano ukhale chete, mlongo wanga, iye ali mlongo wako; usavutika ndi chinthuchi. Chomwecho Tamara anakhala wounguluma m'nyumba ya Abisalomu mlongo wake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Apo Abisalomu, mlongo wa Tamarayo, adamufunsa kuti, “Monga Aminoni uja wakuchimwitsa? Komabe, iwe khala phee, mlongo wanga. Iye uja ndi mlongo wako. Zimenezi usavutike nazo.” Choncho Tamara ankakhala ngati wofedwa kunyumba kwa mlongo wake Abisalomu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Mlongo wake Abisalomu anati, “Kodi Amnoni uja mlongo wako wagona nawe? Khala chete mlongo wanga. Iye uja ndi mlongo wako ndipo usazilabadire.” Choncho Tamara anakhala mʼnyumba ya Abisalomu mlongo wake ngati woferedwa. Onani mutuwo |