Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi
2 Samueli 14:11 - Buku Lopatulika Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mkazi uja adanena kuti, “Chonde, amfumu mupemphe kwa Chauta Mulungu wanu, kuti wolipsira imfa ija asaphenso wina, kuti choncho mwana wanga asaonongeke.” Davide adati, “Pali Chauta wamoyo, mwana wanu sadzapwetekedwa mpang'ono pomwe.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mkaziyo anati, “Mfumu ipemphe kwa Yehova Mulungu wake kuti aletse wobwezera imfa asaphenso wina kuti mwana wanga asawonongedwe.” Mfumu inati, “Pali Yehova wamoyo ngakhale tsitsi limodzi la pamutu pa mwana wako silidzathotholedwa.” |
Ndipo Abramu anati kwa mfumu ya Sodomu, Dzanja langa ndamtukulira Yehova, Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi
Ukasautsa ana anga aakazi, kapena ukatenga akazi kuonjezera pa ana anga, palibe munthu mmodzi ali nafe; taonani, Mulungu ndiye mboni yanga ndi yako.
Ndipo mfumu inati, Ubwere naye kwa ine aliyense wakunena kanthu ndi iwe, ndipo iyeyo sadzakukhudzanso.
Pamenepo mkaziyo anati, Mulole mdzakazi wanu alankhule mau kwa mbuye wanga mfumu. Niti iyo Nena.
Ndipo mfumuyo inanena ndi Yowabu, Taonanitu, ndachita chinthu ichi; chifukwa chake, pita nubwere nayenso mnyamatayo Abisalomu.
Ndipo Solomoni anati, Iye akakhala munthu woyenera silidzagwa pansi tsitsi lake limodzi lonse; koma mukapezeka mwa iye choipa, adzafadi.
Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.
kapena kumpanda ndi dzanja lake momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo akampeza.
nakampeza wolipsa mwazi kunja kwa malire a mzinda wake wothawirako, ndipo wolipsa mwazi akapha wakupha munthu, alibe kuchimwira mwazi;
Momwemo ndikuchenjezani mutenge kanthu kakudya; pakuti kumeneku ndi kwa chipulumutso chanu; pakuti silidzatayika tsitsi la pamutu wa mmodzi wa inu.
Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, kodi Yonatani adzafa, amene anachititsa chipulumutso chachikulu ichi mu Israele? Musatero. Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la pamutu wake lidzagwa pansi, pakuti iye anagwirizana ndi Mulungu lero. Chomwecho anthuwo anapulumutsa Yonatani kuti angafe.
Ndipo Yonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m'dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yako, nthawi zamuyaya. Ndipo iye ananyamuka nachoka; koma Yonatani anamuka kumzinda.
Ndipo Saulo anamlumbirira kwa Yehova, nati, Pali Yehova, palibe chilango chidzakugwera chifukwa cha chinthu ichi.