Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mafumu 1:52 - Buku Lopatulika

52 Ndipo Solomoni anati, Iye akakhala munthu woyenera silidzagwa pansi tsitsi lake limodzi lonse; koma mukapezeka mwa iye choipa, adzafadi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

52 Ndipo Solomoni anati, Iye akakhala munthu woyenera silidzagwa pansi tsitsi lake limodzi lonse; koma mukapezeka mwa iye choipa, adzafadi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

52 Solomoni adati, “Iyeyo akakhala womvera, sitimchita choipa chilichonse, koma akakhala woipa mtima, adzafa basi.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

52 Solomoni anayankha kuti, “Ngati iyeyo aonetse kuti ndi munthu wakhalidwe labwino, ngakhale tsitsi la mʼmutu mwake silidzathothoka ndi kugwera pansi, koma akapezeka kuti ali ndi khalidwe loyipa, adzafa ndithu.”

Onani mutuwo Koperani




1 Mafumu 1:52
11 Mawu Ofanana  

Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.


Ndipo anthu anakauza Solomoni, kuti, Taonani, Adoniya aopa mfumu Solomoni, popeza taonani, wagwira nyanga za guwa la nsembe, nati, Mfumu Solomoni alumbirire ine lero kuti sadzandipha kapolo wake ndi lupanga.


Tsono mfumu Solomoni anatuma anthu nakamtsitsa ku guwa la nsembe. Iye nadza, nagwadira mfumu Solomoni; Solomoni nati kwa iye, Pita kwanu.


Sakhulupirira kuti adzatulukamo mumdima, koma kuti lupanga limlindira.


Chilungamo chitchinjiriza woongoka m'njira; koma udyo ugwetsa wochimwa.


Wolungama aganizira za nyumba ya wamphulupulu, kuti amphulupulu amagwetsedwa, naona zoipa.


komatu inu, matsitsi onse a m'mutu mwanu awerengedwa.


Ndipo silidzaonongeka tsitsi limodzi la pamutu panu.


Momwemo ndikuchenjezani mutenge kanthu kakudya; pakuti kumeneku ndi kwa chipulumutso chanu; pakuti silidzatayika tsitsi la pamutu wa mmodzi wa inu.


Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, kodi Yonatani adzafa, amene anachititsa chipulumutso chachikulu ichi mu Israele? Musatero. Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la pamutu wake lidzagwa pansi, pakuti iye anagwirizana ndi Mulungu lero. Chomwecho anthuwo anapulumutsa Yonatani kuti angafe.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa