Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 4:2 - Buku Lopatulika

2 Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipo udzalumbira, Pali Yehova m'zoonadi, m'chiweruziro, ndi m'chilungamo; ndipo mitundu ya anthu idzadzidalitsa mwa Iye, ndipo mwa Iye adzatamandira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Muzilumbira moona kuti, ‘Pali Chauta wamoyo.’ Muzichita zimenezi mwachilungamo ndi mokhulupirika. Mukatero, anthu a mitundu yonse adzandipempha kuti ndiŵadalitse, ndipo adzanditamanda.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Muzilumbira mokhulupirika ndiponso mwa chilungamo kuti, ‘Pali Yehova wamoyo.’ Mukatero anthu a mitundu ina yonse adzandipempha kuti ndiwadalitse ndipo adzanditamanda.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 4:2
30 Mawu Ofanana  

m'mbeu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mau anga.


Ndipo Solomoni anati, Munamchitira mtumiki wanu Davide atate wanga zokoma zazikulu, monga umo anayenda pamaso panu ndi choonadi ndi chilungamo ndi mtima woongoka ndi Inu; ndipo mwamsungira chokoma ichi chachikulu kuti mwampatsa mwana kukhala pa mpando wake wachifumu monga lero lino.


Dzina lake lidzakhala kosatha, momwe likhalira dzuwa dzina lake lidzamvekera zidzukulu. Ndipo anthu adzadalitsidwa mwa Iye; amitundu onse adzamutcha wodala.


Ndipo mphamvu ya mfumu ikonda chiweruzo; Inu mukhazikitsa zolunjika, muchita chiweruzo ndi chilungamo mu Yakobo.


Ndadzilumbira ndekha, mau achokera m'kamwa mwanga m'chilungamo, ndipo sadzabwerera, kuti mabondo onse adzandigwadira Ine, malilime onse nadzalumbira Ine.


Mwa Yehova mbeu yonse ya Israele idzalungamitsidwa ndi kudzikuza.


chomwecho iye amene adzidalitsa yekha m'dziko lapansi, adzadzidalitsa yekha mwa Mulungu woona; ndipo iye amene alumbira m'dziko lapansi adzalumbira pa Mulungu woona; popeza zovuta zoyamba zaiwalika, ndi popeza zabisalika kumaso kwanga.


Koma Yehova ndiye Mulungu woona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya; pa mkwiyo wake dziko lapansi lidzanthunthumira, ndi amitundu sangapirire ukali wake.


Ndipo padzakhala kuti nditazula iwo, ndidzabwera, ndipo ndidzawachitira chisoni; ndipo ndidzabwezanso iwo, yense ku cholowa chake, ndi yense kudziko lake.


Ndipo padzakhala kuti, ngati iwo adzaphunzira mwakhama njira za anthu anga, kulumbira ndi dzina langa, Pali Yehova; monga anaphunzitsa anthu anga kulumbira pali Baala; pamenepo ndidzamangitsa mudzi wao pakati pa anthu anga.


Inu Yehova, mphamvu yanga, ndi linga langa, pothawirapo panga tsiku la msauko, amitundu adzadza kwa Inu kuchokera ku malekezero a dziko lapansi, ndipo adzati, Makolo athu analandira cholowa cha bodza lokha, zopanda pake ndi zinthu zosapindula nazo.


Pa nthawi yomweyo adzatcha Yerusalemu mpando wa Yehova; ndipo mitundu yonse idzasonkhanidwa kumeneko, ku dzina la Yehova, ku Yerusalemu; ndipo sadzayendanso konse m'kuumirira kwa mtima wao woipa.


Ndipo ndidzayesa mzinda uno chifukwa cha kukondwa, ndi chiyamiko ndi ulemerero, pamaso pa amitundu onse a padziko lapansi, amene adzamva zabwino zonse ndidzawachitirazo, ndipo adzaopa nadzanthunthumira chifukwa cha zabwino zonse ndi mtendere wonse zimene ndidzauchitira.


Ndipo ngakhale ati, Pali Yehova; komatu alumbira monama.


Pakuti mukakonzatu njira zanu ndi machitidwe anu; ndi kuweruzatu milandu ya munthu ndi mnansi wake;


koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.


Ndipo ndidzakutomera ukhale wanga kosatha, inde ndidzakutomera ukhale wanga m'chilungamo, ndi m'chiweruzo, ndi mu ukoma mtima, ndi m'chifundo.


Koma ngakhale tsopano, ati Yehova, munditembenukire Ine ndi mtima wanu wonse, ndi kusala, ndi kulira, ndi kuchita maliro;


ndipo ndidzabwera nao, nadzakhala m'kati mwa Yerusalemu; ndipo iwo adzakhala anthu anga, nanenanso ndidzakhala Mulungu wao, m'choonadi ndi m'chilungamo.


Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu; ndipo m'malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka choona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikulu mwa amitundu, ati Yehova wa makamu.


kuti monga mwalembedwa, Iye amene adzitamanda, adzitamande mwa Ambuye.


Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye;


Ndipo malembo, pakuoneratu kuti Mulungu adzayesa olungama amitundu ndi chikhulupiriro, anayamba kale kulalikira Uthenga Wabwino kwa Abrahamu, kuti, Idzadalitsidwa mwa iwe mitundu yonse.


Muziopa Yehova Mulungu wanu; mumtumikire Iyeyo; mummamatire Iye, ndi kulumbira pa dzina lake.


Mukakhala nao msauko, zikakugwerani zonsezi, masiku otsiriza mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumvera mau ake;


Muziopa Yehova Mulungu wanu; ndi kutumikira Iyeyu; ndipo polumbira muzitchula dzina lake.


pakuti ife ndife mdulidwe, akutumikira popembedza ndi Mzimu wa Mulungu, nadzitamandira mwa Khristu Yesu, osakhulupirira m'thupi;


Gona usiku uno, ndipo kudzali m'mawa, akakuombolera, chabwino, akuombolere; koma ngati safuna kukuombolera, pali Yehova, ndidzakuombolera cholowa ndine; gona mpaka m'mawa.


Ndipo Davide analumbiranso nati, Atate wako adziwatu kuti wandikomera mtima; nati, Yonatani asadziwe ichi, kuti angamve chisoni; koma pali Yehova, ndiponso pali moyo wako, pakati pa ine ndi imfa pali ngati phazi limodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa