1 Samueli 14:45 - Buku Lopatulika45 Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, kodi Yonatani adzafa, amene anachititsa chipulumutso chachikulu ichi mu Israele? Musatero. Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la pamutu wake lidzagwa pansi, pakuti iye anagwirizana ndi Mulungu lero. Chomwecho anthuwo anapulumutsa Yonatani kuti angafe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201445 Ndipo anthuwo ananena ndi Saulo, kodi Yonatani adzafa, amene anachititsa chipulumutso chachikulu ichi m'Israele? Musatero. Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la pa mutu wake lidzagwa pansi, pakuti iye anagwirizana ndi Mulungu lero. Chomwecho anthuwo anapulumutsa Yonatani kuti angafe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa45 Tsono anthu adafunsa Saulo kuti, “Kodi afe Yonatani amene wagwira ntchito yopulumutsa Aisraele kunkhondo? Sizingatheke mpang'ono pomwe. Pali Chauta wamoyo! Tsitsi nlimodzi lomwe la kumutu kwake silipezeka lothothoka. Zimene wachita lerozi, wamthandiza ndi Mulungu.” Motero anthu adamupulumutsa Yonatani, ndipo sadaphedwe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero45 Koma anthuwo anafunsa Saulo kuti, “Kodi Yonatani afe, iye amene wagwira ntchito iyi yayikulu yopulumutsa Aisraeli? Osatheka! Pali Yehova ngakhale tsitsi ndi limodzi lomwe lapamutu pake silidzathothoka, pakuti wachita zimenezi lero ndi thandizo la Mulungu.” Choncho anthuwo anamupulumutsa Yonatani, ndipo sanaphedwe. Onani mutuwo |