1 Samueli 20:42 - Buku Lopatulika42 Ndipo Yonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m'dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yako, nthawi zamuyaya. Ndipo iye ananyamuka nachoka; koma Yonatani anamuka kumzinda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201442 Ndipo Yonatani ananena kwa Davide, Muka mumtendere, popeza tonsefe tinalumbira m'dzina la Yehova, kuti, Yehova adzakhala pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa mbeu yako, nthawi zamuyaya. Ndipo iye ananyamuka nachoka; koma Yonatani anamuka kumudzi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa42 Pamenepo Yonatani adauza Davide kuti, “Pita ndi mtendere, pakuti aŵirife tidalonjezana molumbira m'dzina la Chauta kuti, ‘Chauta ndiye adzakhale mboni pakati pa ine ndi iwe, ndi pakati pa zidzukulu zanga ndi zidzukulu zako mpaka muyaya.’ ” Pompo Davide adanyamuka nachokapo, ndipo Yonatani adabwerera kumzinda kuja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero42 Yonatani anawuza Davide kuti, “Pita mu mtendere pakuti ife awiri tinalumbira mʼdzina la Yehova kuti, ‘Yehova ndiye akhale mboni pakati pa iwe ndi ine ndiponso pakati pa zidzukulu zako ndi zidzukulu zanga kwa nthawi yonse.’ ” Kenaka Davide anachoka, ndipo Yonatani anabwerera ku mzinda kuja. Onani mutuwo |