Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Numeri 35:19 - Buku Lopatulika

19 Wolipsa mwazi mwini wake aphe wakupha munthuyo; pakumpeza amuphe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

19 Wolipsa mwazi mwini wake aphe wakupha munthuyo; pakumpeza amuphe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

19 Mbale wake wa munthu wakufayo ndiye adzaphe wopha mnzakeyo. Akadzangokumana, wopha mnzakeyo adzamuphe ndi munthu wolipsira magaziyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

19 Wolipsira adzamuphanso wakuphayo. Pamene akumana naye adzayenera kumupha ndithu.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 35:19
16 Mawu Ofanana  

Taonani, mwandiingitsa ine lero lomwe padziko; ndi pankhope panu ndidzabisika; ndipo ndidzakhala wothawathawa ndi woyendayenda padziko lapansi; ndipo kudzatero kuti onse akundipeza adzandipha.


Nati iye, Mfumu mukumbukire Yehova Mulungu wanu kuti wolipsa mwazi asaonjeze kuononga, kuti angaononge mwana wanga. Niti iyo, Pali Yehova, palibe tsitsi limodzi la mwana wako lidzagwa pansi.


Ndipo onani, chibale chonse chinaukira mdzakazi wanu, ndi kuti, Upereke iye amene anakantha mbale wake, kuti timuphe chifukwa cha moyo wa mbale wake amene anamupha; koma pakutero adzaononga wolowa yemwe; chomwecho adzazima khala langa lotsala, ndipo sadzasiyira mwamuna wanga dzina kapena mbeu kunja kuno.


Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.


Motero Yowabu ndi Abisai mbale wake adapha Abinere, popeza iye adapha mbale wao Asahele ku Gibiyoni, kunkhondo.


Ndipo mizindayo ikukhalireni yakupulumuka wolipsa; kuti wakupha mnzake asafe, kufikira ataima pamaso pa msonkhano amweruze.


Kapena akamkantha m'dzanja muli chipangizo chamtengo, chakufetsa munthu, ndipo wafa, ndiye wakupha munthu; wakupha munthu nayenso amuphe ndithu.


Ndipo akampyoza momkwiyira, kapena kumponyera kanthu momlalira, kuti wafa;


kapena kumpanda ndi dzanja lake momuda, kuti wafa, womkanthayo nayenso amuphe ndithu; ndiye wakupha munthu; wolipsa mwazi aphe wakupha munthuyo akampeza.


pamenepo msonkhano uziweruza pakati pa wokantha mnzakeyo ndi wolipsa mwaziyo monga mwa maweruzo awa;


nakampeza wolipsa mwazi kunja kwa malire a mzinda wake wothawirako, ndipo wolipsa mwazi akapha wakupha munthu, alibe kuchimwira mwazi;


pamenepo akulu a mzinda wake atumize ndi kumtengako ndi kumpereka m'manja mwa wolipsa mwazi, kuti afe.


kuti wolipsa mwazi angalondole wakupha mnzake, pokhala mtima wake watentha, nampeza, popeza njira njaitali, namkantha kuti wafa; angakhale sanapalamule imfa, poona sanamude kale lonse.


Kuti athawireko wakupha munthu osamupha dala, osadziwa; ndipo idzakhalire inu yopulumukirako, kumpulumuka wolipsa mwazi.


Ndipo akamlondola wolipsa mwazi, asampereke m'dzanja lake wakupha mnzakeyo; pakuti anakantha mnansi wake mosadziwa, osamuda kale.


Ndipo anati, Ndiwo abale anga, ana a mai wanga. Pali Yehova mukadawasunga amoyo, sindikadakuphani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa